‘Covid-19 akweza uchigawenga’
Apolisi ku Mzuzu ati uchigawenga wakula mwezi wa July 2021 kaamba ka mliri wa Covid-19.
Nyengo ngati yomweyi chaka chatha, milandu ya umbanda 660 idachitika mumzindawo koma chaka chino yafika pa 883.
Polankhula pamene polisiyo imasanthula ntchito zake Lachiwiri mkulu wa polisiyo a Fred Chande adati malinga ndi kuima kwa ntchito zina zaima kaamba ka matendawa, anthu ena akulowa uchigawenga kuti apeze loboola.
“Chiwerengero cha odwala ngakhalenso kumwalira kaamba ka Covid-19 chikuchuluka. Enatu achotsedwa ntchito kumene ndipo pofuna kuti moyo upitirire kuyenda, ena alowa uchigawenga,” adatero iwo.
Iwo adati milandu yokhudza za chiwerewere nayo yakwera mumzindawo nthawi imeneyi.
“Pajatu ena sakuyenda ndiye akukhalitsa ndi ana, zimene zachititsanso kuti azigona ndi anawo. Milanduyi ikuchuluka,” adatero iwo.
Koma iwo adati apolisi akuyesetsa kuyendayenda mumzindawo komanso kulimbikitsa mgwirizano ndi anthu okhala kumeneko, osaiwala ena okhudzidwa.
Wachiwiri kwa wapampando wa komiti ya papolisiyo a Angela White adagwirizana ndi a chande ndipo adati komiti yawo imene mulinso nzika ndi apolisi, ikumana kuti mavutowa n’kuthana nawo bwanji.