Mphunzitsi asamutsidwa atagona ndi mwana
Mbwanamkubwa (DC) wa boma la Nsanje a Medson Matchaya wapempha komiti ya chitukuko kwa T/A Malemia m’bomalo kuti afufuze nkhani ya mphunzitsi wina amene akumuganizira kuti adagona ndi wophunzira wake mpaka kumupatsa mimba.
Izi zidatomphoka pamene bungwe la Centre for Alternatives for Victimised Women and Children (Cavwoc) lidabweretsa pa mbalambanda nkhanza zimene zikuchitika m’bomalo.
A Matchaya adapereka sabata ziwiri kuti komitiyo ilondoloze nkhaniyi chifukwa mphunzitsiyo (sitimutchula dzina) atapereka mimba kwa mwanayu adapempha kuti apite sukulu ina kuti nkhani izizire.
“Mphunzitsiyo ayenera kuimikidwa ntchito kuti afufuzidwe. Inu a ADC nkhaniyi muyenera kuitsata mpaka mutu wake uoneke,” adatero a Matchaya.
Malinga ndi mmodzi mwa amene adachita nawo kafukufukuyo ochokera ku Cavwoc a Mary Namalomba, n’zachisoni kuti aphunzitsi ena akukhudzidwa ndi nkhani zogona ndi ana a sukulu ndipo mmalo molandira chilango choyenera akungosamutsidwa.
Mkulu wa zachisamaliro cha anthu ku Nsanje a Chikumbutso Salifu, adati aonetsetsa kuti nkhani ya mphunzitsiyo itsatidwe bwino mpaka kumapeto kuti ngati angapezekedi olakwa ndi bwalo la milandu akasewenze.
“Iwo monga mphunzitsi, anali ndi udindo waukulu kuteteza ophunzira. Kusandutsa mwana wa sukulu kukhala mkazi wake n’kuphwanya malamulo komanso kumuphera mwanayo ufulu wake wa maphunziro. Apolisi alowererepo,” adatero iwo.
Mkulu wa zamaphunziro ku Nsanje a Grestone Alindiamawo nawo adati atsatira malamulo ndipo aonetsetsa kuti chilungamo chiyende ngati madzi.
A Matchaya adati palinso aphunzitsi atatu amene kafukufuku wa bungwelo adaonetsa kuti nawonso adagona ndi ophunzira awo ndipo nkhanizo akuzifufuzabe.
Imodzi mwa nkhani zimene zidapatsa chidwi anthu patsikulo ndi ya mlonda wina pachipatala chaching’ono cha Chididi amene akuti amagwira amayi ziwalo zobisika ati pofuna kuwayeza ngati nthawi yawo yakwana.
Mmodzi mwa amayi amene adachitiridwa izi [sitimutchula dzina] adati mlondayo amalandira amayi oyembekezerawo akafika ndi kuwalozera malo oti agone.
“Kupereka malo ogona kwa amayi amachitako n’kolakwa chifukwa si ntchito yake. Nanjinanji izi zowagwira amayiwo malo obisika n’kuphwanya ufulu wawo. Ameneyu ayeneranso kufufuzidwa,” adatero a Matchaya.
Kudatuluka nkhani zina monga za aphunzitsi amene akumathawa ntchito yawo n’kumakayendetsa njinga za kabaza kuti apeze loboola.
Malinga ndi wapampando wa Malemia Area Development Committee (ADC) a Matthias Chilumba, zidali zonyaditsa kuti kafukufuku wa Cavwoc watumphula nkhanza zimene zikuchitika m’deralo zomwe mmbuyomu zikadabisidwa.
“Tionetsetsa kuti unduna wa maphunziro uchotse mphunzitsiyo ndipo apolisi agwire ntchito yawo. Tikuthokoza a Cavwoc chifukwa chobweretsa nkhani zotere pa mbalambanda makamaka pa nkhani zoti adindo aziphwanya ufulu wa ena,” adatero a Chilumba.