Nkhani

DPP idyera Khrisimasi m’khoti

Woweruza ku bwalo la milandu lalikulu ku Lilongwe a Justice Howard Pemba ati adzapereka chigamulo chawo pa 26 December 2023 pa nkhani yomwe akuluakulu atatu a komiti yaikulu ya chipani cha Democratic Progressive (DPP) adachikokera kukhoti.

Izi zikutanthauza kuti otsatira chipani cha DPP adya Khrisimasi ya chaka chino Lolemba likudzali mitima ili dyokodyoko ndi nkhawa kulingalira momwe chigamulocho chidzakhalire pa Khrisimasi bokosi.

A Nankhumwa adakamang’ala kukhoti

Akuluakulu atatuwo a Kondwani Nankhumwa, a Cecilia Chazama komanso a Grezelda Jeffrey akupempha khothilo kuti liletse zonse zomwe chipani cha DPP chidakambirana kumsonkhano wakomiti yayikulu pa 13 December 2023 kunyumba kwa mtsogoleri wachipanicho a Peter Mutharika.

Kumsonkhanowo, komitiyo idagwirizana kuti chipanicho chidzakhale ndi msonkhano wosankha atsogoleri wa konvenshoni pa 26 ndi pa 27 December 2023 komanso kuti a George Chaponda ndiwo adzayendetse komvenshoniyo.

Izi zimatsatiranso kuti chipanicho chidakatenga chiletso kuti zomwe gulu linanso la komiti yomweyo yomwe ili mbali ya a Nankhumwa zidagwirizana zisagwire ntchito chifukwa msonkhanowo sudali ovomerezeka.

Ku msonkhano uwu, komitiyo idagwirizana kuti komvenshoni idzachitike pa 15 ndi pa 16 December 2023 ku Natural Resources College (NRC) ku Lilongwe ndipo adzayendetse komvenshoniyo ndi a Nicholas Dausi.

Pamlandu womwe akuyembekezerawo, akuluakulu atatuwo akupemphanso khothi kuti lilamule mtsogoleri wachipanicho a Mutharika ndi chipani chonse kuti awabwezeretse m’mipando yawo yakale yomwe adasankhidwa ku konvenshoni ya 2018.

Komiti ya pambuyo pa a Nankhumwa itachita msonkhano wake omwe adaitanitsa ndi yemwe adali mlembi wa chipanicho mayi Grezelda Jeffrey, a Mutharika adasuntha mamembala atatuwo m’maudindo awo ati pogwiritsa ntchito mphamvu zawo kuchipani.

Iwo adachotsa a Jeffrey ngati mlembi wamkulu n’kuwapatsa udindo wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani pachigawo cha pakati ndipo udindo wawo adaupereka kwa a Clement Mwale pomwe a Nakhumwa adawachotsa pampando wa wachiwiri kwa pulezidenti wa chipani kuchigawo cha kummwera n’kuwapatsa udindo wa mlangizi wa a Mutharika.

Udindo wa a Nankhumwa adaupereka kwa a George Chaponda pomwe a Chazama atawachotsa pa mpando wa woyang’anira amayi m’chipani n’kuwapatsa waulangizi wa a Mutharika, mpando wawo adaupereka kwa mayi Mary Navicha.

Malingana ndi mlangizi wachipani cha DPP pa zamalamulo a Charles Mhango, zomwe khoti lidanena Lachiwiri zikutanthauza kuti mpakana pa 26 December 2023, atatuwo akadali m’mipando yawo yatsopano yomwe akuikanayo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button