Chichewa

HRDC yawonanji m’boma la Tonse

Anthu ambiri akhala akudabwa kuti gulu lomwe lakhala likutsogolera Amalawi pa ziwonetsero zokhudza kusagwirizana ndi momwe boma likuyendera la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) lili kuti? Gululi lidapanga mbiri chifukwa chakupanda mantha podzudzula utsogoleri pa zomwe zikulakwika. Mbiriyi ili apo, chilowereni boma latsopano la Tonse Alliance, gululi lakhala chete kwa nthawi yaitali moti ena adayamba kulingalira kuti lidatha. Komatu m’sabatayi gululi lidatulutsa liwu lake loyamba lomwe silikuluma kapena kuuzilira bala. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi wapampando wa gululi Gift Trapence kuti asanthule momwe boma la Tonse Alliance likugwirira ntchito.

Trapence: Tonse Alliance yapeza 50 pa 100

 A Trapence choyamba talongosolani bwino kuti n’chifukwa chiyani HRDC yachita phee pakatipa?

M’bale wanga ndikhulupirira umatitsatira bwino ife a HRDC kuti sitingolubwalubwa paliponse pokhapokha pakhale zakupsa. Anthu akhoza kuona ngati takhala phee pa zifukwa zobooka m’mutu koma ayi ndithu ntchito ikuyenda. Monga mukudziwa kuti tili mu ulamuliro watsopano, takhala phee chifukwa timaunika kuti kodi nzeru za Tonse Alliance n’zotani. Kodi atithandiza kapena ayi? Timawaunika kaye kuti tikayamba kuwatambasula, tizikamba zomwe anthu akuona ndi kudziwa.

Ndiye poti mwayamba kubwera poyera, tiziti mwaonanji mwa boma la Tonse Alliance?

Padakalipano taona kuti n’chithumba cha kasakaniza. Muli zambiri zakupsa, komasno muli zaziwisi. Inde tikudziwa kuti angoyamba kumene ndipo n’zosatheka kukwaniritsa zonse komanso ifeyo tidaona kuti n’kwabwino kupereka chithunzithunzi cha momwe zinthu zikuyendera patatha miyezi imeneyi kuti Amalawi adziwe zomwe zikuchitika komanso kuti akuluakuluwo adzigunde pamtima n’kuona kuti zofowoka zawo n’ziti ndipo angazikonze bwanji, komanso zomwe akupanga bwino n’ziti kuti apitirize.

Chabwino ticheze motere, taona bomali likumanga n’kuyamba kufufuza ena mwa akuluakulu omwe adali m’boma la kale pa milandu yosiyanasiyana ndipo ena akuti n’kungofuna kupha chipani cha DPP, pamenepa inu mukuonapo bwanji? Nanga boma silikuphwanya ufulu wa anthu?

Ayi silikuphwanya ufulu wa anthu, komano imeneyi ndi mbali imodzi ya zomwe bomali likuchita bwino. Inu mukudziwa zomwe zidaululika boma litangosintha kuti anthu amakolola posalima m’boma ndipo mudali katangale wadzawoneni ndiye bomali pomwe limachita kampeni lidalonjeza kuti zonsezo lidzathana nazo ndipo lidzaonetsetsa kuti lalondoloza ndalama zomwe zidabedwa m’boma. Njira yake ndi imeneyi. Akuyenera kukoka angapo kuti afukule bwino ndipo akawapeza osalakwa, tonse timadziwa momwe zimakhalira koma akawapeza olakwa ndiye kuti alondola komwe kuli ndalama za boma n’kuzibweza. Mbali imeneyi asiyeni koma kuti asamagwire mbali imodzi ayi ngakhale omwe ali m’boma la Tonse Alliance akalakwa azitengedwa.

Nanga za zipangizo zotsika mtengozi inu mwaziunika motani?

N’zowona mu ntchito yogulitsa zipangizozi mukuchitika zambiri, koma nkhani yomwe tikhazikikepo ndiyoti kodi zomwe boma lidalonjeza zikuoneka kapena ayi? Ndanena izi chifukwa mukakumbukira padzana, boma linkapereka zipangizo kwa anthu 900 000 kapena 1 miliyoni akachuluka, koma pano tikukamba za 4.2 miliyoni komanso adatiuza kuti anthu azidzagula pa mtengo wa K4 495 pa thumba la 50kg ndipo n’zomwe zikuchitika. Ndifotokoze momveka bwino kuti bungwe la HRDC silidabadwe kuti lizingosaka zofooka ayi, komanso kuunikira ndikumenyera Amalawi ufulu ndiye n’chifukwa chake pomwe zina zikuyenda bwino timanena komanso zikalakwika timadzudzula. Apapa ngakhale padali mavuto ena mu ntchito yogawa zipangizo zotsika mtengo timvetsetsa chifukwa chiyambi n’chovuta koma tsogolo lokwaniritsa lonjezo likuoneka.

Zabwino zina mwaonako n’ziti?

Ndikhulupirira mwayamba kale kuona kuti msonkho pa malipiro anu akudula kuyambira K100 000 m’malo mwa K45 000 yakale, apa ndi mpumulo kwa Amalawi tiyamikile. Palinso nkhani iyi ya lamulo loti anthu azitha kupeza nkhani mosavuta (Access to Information) yomwe yakhala ikuponderedzedwa zaka zambiri itavomeredwa kale ku Nyumba ya Malamulo, koma awa asayinira kuti liyambe kugwira ntchito. Lamulo limeneli sitimalifuna ndife tokha Amalawi ayi, koma ngakhale maiko ndi mabungwe omwe amatithandiza akhala akupempha kuti lamuloli liyambe kugwira ntchito ndipo layamba. Pali zambiri zoti titha kukambirana mpaka dzuwa kulowa.

Zomwe mwaonapo mavuto n’ziti?

Popeza tangoyamba kauniuni wathu pali zingapo zomwe taonamo zofooka monga zija takambirana kale za zipangizo zotsika mtengo kuti kwina zikuyenda bwino, koma tidzudzule apopo poti anthu mpaka kumagona kogula fetereza ndi mbewu ayi sizikuyenera kutero. Apapa zikuonekabe kuti ngakhale lonjezo la mtengo ndi chiwerengero cha anthu opindula zikuoneka kusintha, ntchito yayamba mogwedera kwambiri moti ndi pempho lathu kuti komwe tikuloweraku zinthu zisinthe zisamayende ngati momwe zayendera chaka chino.

Mwachindunji bomali mungalipatse malikisi otani ndipo mpazifukwa zingati?

Ndilipatsa 50 pa 100 chifukwa zikuoneka kuti kwina zikuyenda ngakhele kwina zikugwedera. Mlingo weniweni ndidzapereka mtsogolo muno nthawi ikadutsa kuti tikhoza kupereka mlingo weniweni koma padakalipano tikhazikike pamenepa pakuti zinthu zikuyenda pa theka la muyeso. Ndikambeko pa mawu mudanena koyambirira aja kuti anthu akuona ngati tidazizira, ayi Amalawi asasiye kutidalira ndikutikhulupirira chifukwa tili pano kuwamenyera nkhondo yoti azitha kusangalala ndi ufulu wawo omwe malamulo amawapatsa. Sitidzagona pomwe Amalawi akuphula njerwa zamoto ayi apo ndiye sitingalole.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button