Nkhani

Kugula feteleza wotsika kwayambika

Listen to this article

Amalawi ena ayamba kugula feteleza ndi mbewu zotsika mtengo koma madera ena ngakhale maina a opindula pa chilinganizochi sanadziwike.

Sabata imene ikuthayi Amalawi amene ali m’kaundula wa unduna wa malimidwe adayamba kugula matumba awiri a feteleza pamtengo wa K4 495 thumba lililonse komanso mbewu yolemera makilogalamu 5 pamtengo wa K2 000. Alimi 4.2 miliyoni akuyembekezera kugula zipangizo zotsika mtengozi malinga ndi chilinganizo cha boma.

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera adakhazikitsa ndondomekoyo pa 17 October

Kafukufuku wathu adasonyeza kuti maboma monga a Blantyre, Phalombe komanso Zomba ndi omwe ayamba kugula zipangizozi.

Woyang’anira ndondomekoyi kuunduna wa zaulimi Justine Kagona adati undunawu ukuonetsetsa kuti alimi athe kupeza zipangizo zotsika mtengozi m’nthawi yake.

“Alimi amaboma ena ayamba kugula zipangizozi sabata ino koma maboma monga Mwanza adakumana ndi mavuto okhudzana ndi anzathu omwe amagulitsa zipangizozi koma tili ndi chiyembekezo choti alimi ayamba kugula zipangizozi pa 26 October,” adatero Kagona.

Poonetsetsa kuti ndondomekoyi yawafikira alimi onse munthawi yake undunawu walangiza omwe amayendetsa ntchito zaulimi maboma onse kuti asanayambe kugulitsa zipangizozi aziyamba afananitsa mayina akafika pa 95 pa maina 100 omwe akuyenera kupindula ndi ndondomekoyi.

Koma ku Number 1 m’boma la Thyolo ntchitoyi yayamba ndi zotsamwitsa pomwe anthu ena adagona kumalo ogulitsirako zipangizo  poyembekeza kuti ayamba kugulitsa.

Izi zidachitika chifukwa netiweki kusitolo zogulira zipangizozo siyimagwira. Netiwekiyo ndi yothandiza kuti anthu amene agula ndi kuonetsa chitupa cha unzika asakayesere kugulanso kwina

Anthuwa adali ochoka ku Thyolo Thava m’dera la pakati m’bomalo komanso kumadzulo kwa bomalo komwe zipangizozi sadayambe kugulitsa.

Polankhulapo, khansala wa dera la Nchima, m’dera la pakati m’boma la Thyolo Hudson Ovira khamu lina la anthu lidakagona pakhomo pake pomwe a kampani ya Zathuzathu akugulitsirapo zipangizo.

“Kuno zinthu zayamba koma poti chilichonse chikamayamba, sipalephera zovuta, zinthu zake zikuyenda mwa pang’onopang’ono, akungogulitsa anthu ochepa chabe n’kuima,” adalongosola Ovira.

Koma ngakhale mafumu ena akuti maina a anthu opindula pa chilinganizochi adziwika kuchokera kuboma, mafumu ena akuti kaundulayo sanafike kuchokera kuboma. Mwa mafumu omwe tinacheza nawo, Mfumu Mwangitsa kwa T/A Symon ku Neno komanso T/A Mwankhunikira ya ku Rumphi adati zonse zili tayale pomwe mfumu Nthole ya ku Nsanje, mfumu Nkwata ya ku Thyolo ndi Mwenelufita ya m’boma la Chitipa ati akadayang’anira kunjira.

Polankhula ndi Tamvani Lachinayi, Mwenelufita adati ndi wokhumudwa ndi momwe ndondomekoyi yayambira kwawoko chifukwa ngakhale sanaldnire mndandanda wa amene apindule pachilinganizochi, sitolo zina zayamba kale kugulitsa zipangizo.

“Izi zichititsa kuti chilinganizochi chisokonekere chifukwa anthu ochokera ku Zambia ndi Tanzania akhonza kugula feteleza wotsikayu,” adatero iye.

Mwangitsa adati chilinganizo cha chaka chino chili bwino chifukwa anthu amene adatuluka m’kaundula wokagula mbewu ndi feteleza tsopano chakula.

“Mmbuyomu timakhala pa mavuto chifukwa olandira amakhala ochepa kwambiri choncho anthu anayi amagawana thumba limodzi. Malinga ndi mndandanda umene talandira kuchoka ku unduna wa malimidwe, zikuoneka kuti ambiri apindula ndithu,” adatero Mwangitsa.

Mwankhunikira adati zinthu zili tayale m’dera lake ndipo akungodikira katundu kuti afike kuchokera ku Mzuzu.

Iyo idati maina a mabanja pafupifupi 3 000 omwe akuyembekezera kupindula m’ndondomekoyi ali kale mmalo mwake.

Malinga ndi Mwenelufita, anthu ake akudikirabe maina a amene apindule pa chilinganizochi chifukwa poyamba adasokonekera pomwe dzina ndi nambala ya pachiphaso sizimagwirizana.

“Komanso katundu sadafike. Kunena zoona, chaka chino zachedwa ndipo maso athu ali kunjira,” adatero Mwenelufita.

Boma lidaika padera K160 biliyoni m’ndondomeko ya chuma, kuchokera pa K36 biliyoni ya chaka chatha ndipo chiwerengero cha anthu opindula chakwera kuchoka pa 900 000 kufika pa 4.2 miliyoni.

Related Articles

Back to top button
Translate »