Nkhani

Kuberana pafoni kukupitirirabe

Listen to this article

Ngakhale dziko lino lidakhazikitsa malamulo othana ndi kuberedwa pogwiritsa ntchito njira zamakono monga lamya ndi kompyuta, anthu akuberedwabe.

Masiku apitawa amayi awiri ovutikitsitsa ochokera m’mudzi mwa Ndelema, kwa T/A Kachindamoto m’boma la Dedza akadaberedwa ndalama zomwe adalandira za mtukula pakhomo.

Mmodzi mwa amayiwo, Ellen Kadaluka adati atangolandira ndalama yake ya mtukula pakhomo yokwana K35 000 pa 2 October, nthawi yomweyo adalandira lamya kuchokera kwa munthu wosamudziwa yemwe adamuuza kuti amupatse K10 000 ndipo ngati satero, amuchotsa pamndandanda wa anthu opindula ndi mtukula pakhomo.

“Aka n’koyamba ine kulandira mtukula pakhomo ndipo izi zidandipatsa mantha. Anandiuza kuti ndalama mwalandirayo, mundithokoze ndi K10 000. Koma ine ndidadziwa kuti ndi wakuba ndipo sindidawapatse,” adalongosola Kadaluka.

Pomwe Mirriam Frank wa m’mudzi omwewo adati adali odabwa kuti anthuwo adadziwa bwanji kuti adalandira ndalama za mtukula pakhomo.

Amalawi ambiri akhala akuberedwa podzera njra ngati zimenezi ngakhale pali lamulo la Electronic Transactions and Cyber Security lomwe zina mwa zolinga zake ndi kuthana ndi umbava wa palamya kapena makina a kompyuta. Lamuloli lidakhazikitsidwa m’chaka cha 2017.

Malinga ndi lipoti la chaka chino lomwe lidasindikizidwa mu Financial Crime News lotchedwa Malawi Deep Dive 2020, anthu ambiri ali pachiopsezo choberedwa pogwiritsa ntchito lamya m’dziko muno.

Lipotilo lidati pakufunika njira zokhazikika zoonetsetsa kuti anthu sakuberedwa palamya.

Mkulu wa bungwe la akatakwe pa nkhani za makompyuta ndi lamya la ICT Association of Malawi(Ictam) Bram Fudzulani adati akubawa akumapezerapo mpata pa umbuli ndipo izi ndi zomwe zikukulitsanso mchitidwewu.

Fudzulani adati mpofunika anthu aphunzitsidwe kwatunthu momwe angatetezere ndalama zawo.

Malinga ndi banki ya Reserve Bank of Malawi (RBM), chiwerengero cha anthu omwe amagwiritsa ntchito lamya potumiza ndi kulandira ndalama m’dziko muno n’chopitirira 1 miliyoni. Pomwe anthu oposa 7.2 miliyoni ndiwo ali ndi lamya za m’manja.

Related Articles

Back to top button
Translate »