Nkhani

Kupewa nsabwe za m’fodya ndi pano

Listen to this article

Nsabwe za mufodya ndi gwero limodzi lomwe limachititsa kuti fodya avute malonda kumsika ndipo vutoli likagwera mlimi, chaka chimenecho amalirira kuutsi kaamba koti ngati ogula sadagule fodyayo pamitengo yolira ndiye kuti wabwezedwa.

Malingana ndi katswiri wa zafodya, vutoli ndi lopeweka ndipo kapewedwe kake n’kosabowola m’thumba poyerekeza ndi zomwe zimalowa pofuna kupulumutsa fodya nsabwezo zikalowa.TOBACCO

Mkulu wa bungwe la alimi a fodya la Tobacco Association of Malawi (Tama), Reuben Maigwa, wauza Uchikumbe kuti vuto lalikulu la nsabwe za mufodya ndi lakuti zimateketa fodya nkukhala ngati wagayidwa kale ndiye ukapita kumsika, ogula sachita naye chidwi.

“Ogula fodya amayang’ana mtundu, makulidwe ndi kukhuthala kwa masamba a fodya, osati ufa wa fodya, ayi. Ndiye amati akatsegula belo n’kuonamo ufa amaona ngati ndi fodya wachinyengo ndipo amamubweza. Zikatero ndiye kuti chaka chimenecho zadapo,” adatero Maigwa.

Iye adati nthawi yopewa vuto la nsabwe za mufodya ndi ino poti ikayambika ntchito yothyola fodya mpata umasowa komanso zimathandiza kuti nsabwezo zisakhale ndi mpata wokwanira oswana.

Mkuluyu adati nthawi zambiri gwero la nsabwezi limakhala zipangizo zomwe zidagwiritsidwa ntchito chaka chinzakecho zomwe zidakhudzidwa ndi nsabwe kapena malo osungiramo fodya panthawi yoyembekezera kupita kumsika.

“Tikunena pano, alimi ena adayamba kale kusonkhanitsa zipangizo ngati ziguduli zodindira mabelo, ulusi wosokera ndi zipangizo zina ndipo zimenezi ndizo zimatha kuyambitsa nsabwe ngati komwe zidagwira ntchito mmbuyomo kudali vuto la nsabwe.

“Kupewa kwake n’kosavuta chifukwa choyenera nkuchapa zipangizo zoterezi bwinobwino n’kupopera mankhwala usadasunge pamalo abwino kudikira ntchito yake,” adatero Maigwa.

Iye adati kuchapa ndi kupopera kokha sikukwanira ngati malo osungiramowo sali osamalika chifukwa nsabwezo nthawi zina zimatsakamira m’makoma ndiye ngakhale zipangizo zitasamalidwa bwino n’kusungidwa m’malo omwe muli nsabwe palibe chomwe chachitika.

“Chaka chilichonse malonda a fodya akatha timayenera kutsuka makoma onse a momwe timasungiramo fodya wathu ndi pansi pomwe n’kupoperamo makhwala kuti tizilombo ngati nsabwe tife,” adatero Maigwa.

Iye adati alimi ambiri amagwa m’mavuto ndi nsabwe za fodya kaamba kolekerera n’kumaganiza kuti nthawi idakalipo kenako akaona kuti zawakoka manja amayamba kuchita zachidule ntchito n’kumaonongeka.

“Fodyatu sachedwa, posachedwapa ena ayamba kuthyola ndiye ikangofika nthawi imeneyi mpata umasoweratu chifukwa umati mmawa uli kothyola, masana ukusoka uku ukupachika m’mikangala ndiye zoti ungapeze mpata wokachapa ziguduli kapena kukakonza mosungira mpovuta,” adatero katswiriyu.

Maigwa adatiso nthawi yomwe ino ndiye yofunika kuyambapo kukonza zigafa ngati zidaonongeka kapena ngati palibiretu kuti pomwe fodya azidzachoka kumunda kubwera kumudzi adzakhale ndi pofikira, osati zomwe amachita ena zopachika fodya m’khitchini mophikira chifukwa chosowa malo osungiramo fodya.

Iye adati fodya ali ndi kaumitsidwe kake komwe kamapangitsa kuti akhale wopatsa chikoka, wopanda madontho komanso wafungo la fodya weniweni chifukwa si fodya yense yemwe amalira kutchisa. n

Related Articles

Back to top button
Translate »