Nkhani

Kutambasula nthenda ya kadzamkodzo

Listen to this article

Kunjaku kuli nthenda zosiyanasiyana koma nthenda zina ukamva, kudulitsa mutu wazizwa. Sabata yapitayi, nduna ya zaumoyo, Dr Peter Kumpalume, adatsogolera Amalawi kutsegulira nyengo yokumbukira matenda a kadzamkodzo (Fistula) m’boma la Kasungu. STEVEN PEMBAMOYO adachita chidwi ndi nthendayi ndipo adacheza ndi ndunayi, yomweso idagwiraponso ntchito ya udokotala, kuti itambasule za nthendayi motere:

Kumpalume kutsindika za vuto  la kadzamkodzo
Kumpalume kutsindika za vuto la kadzamkodzo

Anduna, anthu akudziweni.

Ndine Dr Peter Kumpalume, nduna ya zaumoyo, komanso phungu wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) kudera la kumadzulo kwa boma la Blantyre. Ndagwirapo ntchito zachipatala m’madipatimenti osiyabnasiyana m’dziko muno ndi maiko akunja.

Kodi apa mukuti pakuchitika zokhudza kadzamkodzo, chimenechi n’chiyani?

Iyi ndi nthenda yoopsa kwambiri koma anthu ambiri sazindikira. Nthenda imeneyi imagwira amayi ndipo mzimayi akagwidwa ndi nthenda imeneyi, moyo wake umasinthiratu. Amadutsa m’chipsinjo chachikulu, makamaka chifukwa chosalidwa ndi amayi anzake ngakhale abambo apakhomo, moti ena banja mpaka limatha.

Amasalidwa m’njira yanji, kapena matendawa ndi opatsirana?

Ayi, matendawa si opatsirana koma amayamba malingana ndi zichitochito zina pamoyo wa munthu, makamaka pazokhudzana ndi uchembere. Mayi amagwidwa ndi matendawa malingana ndi momwe wayendetsera moyo wake wa uchembere, koma palibe mwayi woti wina akagwidwa akhoza kupatsira anzake, ayi.

Ndiye chomusalira n’chiyani?

Poyamba mukuyenera kumvetsetsa kuti nthendayi ndi nthenda yanji ndipo imachita zotani. Imeneyi ndi nthenda yokhudza njira ya amayi. Pazifukwa zina, njirayi imapezeka kuti yabooka ndiye mkodzo ukamabwera umangodutsa n’kumachucha, mwinanso n’kusakanikirana ndi chimbudzi. Pachifukwachi, mzimayi amamveka fungo kwambiri moti pagulu la anzake amasowa mtendere komanso anzake amamuthawa. Chomwechomwechonso, abambo a kunyumba amatha kupirira kwa kanthawi koma pena amatopa n’kuchoka pakhomopo. Si nkhani yamasewera, ayi, makamaka kwa mayi yemwe wagwidwa ndi matendawo.

Mwangoti pazifukwa zina, kodi simungatambasuleko zina mwa zifukwazo?

Ndikufotokozerani zifukwa zitatu zomwe ndi zikuluzikulu muno m’Malawi. Pali uchembere olawirira. Munthu akatenga pakati ali wamng’ono, ziwalo zake zimakhala kuti sizidakhwime ndiye chifukwa chokakamiza pobereka, vuto lotere likhoza kubwera. Njira ina n’kubereka pafupipafupi, ziwalo zimatopa mpaka nthawi imadzakwana yoti vuto laonekera komanso njira ina ndi kukonda kuchirira kwa azamba chifukwa pakabwera vuto panthawi yochira, azamba amalephera machitidwe ake.

Ndiye mwati vutoli ndi lalikulu m’dziko muno, palibe njira yothandizira amayi oterewa?

Njira ilipo yomwe nkuthamangira kuchipatala basi. M’dziko muno muli zipatala zingapo komwe kuli madipatimenti othandiza pavutoli koma anthu ambiri amatsogoza kuti matendawa amabwera kaamba kolodzana moti amataya nthawi n’kumayendayenda mwa asing’anga mmalo moti athamangire kuchipatala akalandire thandizo zinthu zisadafike poipitsitsa.

Nanga kungoti zipatala, osatiuzako kuti ndi kuti kuli zipatalazo?

Zina mwa zipatala zomwe zikupereka nawo thandizo kwa amayi omwe ali ndi nthendayi ndi Queen Elizabeth Central Hospital (Quech) mumzinda wa Blantyre, Zomba Central Hospital ku Zomba, Bwaila ku Lilongwe, Mzuzu Central Hospital ndi Monkey Bay.

Kadzamkodzo amapha kapena vuto n’kusalidwako basi?

Mwafunsa fuso labwino kwambiri lomwe anthu ambiri amalilambalala. Choyamba dziwani kuti moyo wa munthu umayenda bwino ndi magawo osiyanasiyana ndipo mtendere wa mumtima ndi limodzi mwa magawowo. Munthu yemwe akusalidwa pachifukwa china chilichonse, moyo wake suyenda bwino ngakhale atamadya bwino motani. Ndikhulupilira apa mwamvetsetsa kuopsa kwa nthendayi. n

Related Articles

Back to top button