Nkhani

La 40 lakwana kwa womata anthu phula

Listen to this article

Wakhala akumata anthu phula m’midzi kuti amupatse ndalama ndipo adzakhala ndi mwayi wopeza ngongole kuchokera ku bungwe la Emmanuel International.

Midzi 21 ya kwa gulupu Makumba ndi Mtaka ikulirira ku utsi atawakwangwanula ndalama dzuwa lili gee!

La 40 lamukwanira Wyson Mandolo wa zaka 36 pamene bwalo la milandu m’boma la Mangochi lamupeza wolakwa ndipo akukaseweza zaka ziwiri ndi kugwira ntchito ya kalavula gaga.

Wapolisi wotengera milandu kubwalo m’bomalo, Maxwell Mwaluka, adauza bwalolo kuti kuyambira mwezi wa May mpaka June chaka chino, Mandolo wakhala akumayenda m’midzi kumanamiza anthu kuti amagwira ntchito ku bungwe la Emmanuel International kwa mfumu Chowe.

Lachiwiri pa 10 July, Mwaluka adauza bwalo kuti m’njira iyi, Mandolo adawabera anthu K130 000 powanamiza kuti adzapatsidwa ngongole kudzera m’mabanki m’khonde.

Wachiwiri kwa mneneri wapolisi ya Mangochi, Amina Daudi adati Mandolo adakwanitsa kutolera K6 000 kwa gulu lililonse m’midzi 21.

“Iye amaimbidwa milandu iwiri, womata phula anthu komanso kunama kuti amagwira ntchito ku bungwe la Emmanuel International ndipo milandu yonseyi adaivomera,” adatero Daudi.

“Woweruza mlanduwo, Ronald M’bwana, adapereka ziwiri kundende pa mlandu uliwonse ndipo akakhala kundende zaka ziwiri zokha,” adaonjeza Daudi.

Mandolo amachokera m’mudzi mwa Mwachande kwa mfumu yaikulu Mkanda m’boma la Mulanje.

Related Articles

Back to top button