Chichewa

Madzi achita thope ku DPP

Listen to this article

 

 

Madzi sakudikha kuchipani cha DPP pamene mpungwepungwe wolimbirana amene adzatsogolere chipanichi ku chisankho cha 2019 wafika pa kamuthemuthe.

Atsogoleri ena a chipanichi anenetsa kuti kaya wina afune kaya asafune, amene atsogolere chipanichi ndi mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika basi, osati wachiwiri wake Saulos Chilima monga ena akufunira. Ofuna Chilima akuti Mutharika, yemwe ali ndi zaka 79, wakalamba ndipo sangadzapambanitse chipanicho pachisankho cha chaka chamawa.

Ena akufuna Mutharika (Kumanja) pomwe ena kuti koma Chilima

Mkokemkokewu ukudabwitsa kadaulo wandale ku Chancellor College, Ernest Thindwa amene akuti izi zimayenera zikachitike kumsonkhano waukulu.

Iye adati akuluakuluwa akuyenera kuchita manyazi chifukwa izi zimatuluka kumsonkhano waukulu osati zomwe zikuchitikazi.

“Ngati chipanicho chili cha demokalase, ndiye sakuyenera kubwera kale ndi mtsogoleri wawo pokhapokha msonkhano waukulu utachitika. Amene akusankha APM akuyenera kuchita manyazi chifukwa izi zikusemphana ndi ndale za demokalase,” adatero Thindwa.

Lachiwiri m’sabatayi, wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanicho m’chigawo cha kummwera, George Chaponda adati Mutharika akadutsa kumsonkhano waukulu popanda wopikisana naye.

Naye mneneri wachipanicho Nicholas Dausi adati wina afune kaya asafune koma Mutharika ndiye atsogolere chipanichi m’chisankho cha 2019.

“Tichititsa msonkhano waukulu womwe ukasankhe mtsogoleri, koma wathu ndi Mutharika basi,” adatero Dausi. “Akupitiranji kumsonkhano waukulu pamene asankha kale mtsogoleri?” zikudabwitsa Thindwa.

Mlembi wa chipanichinso Greselder Jeffrey adati kaya ‘satana afune kaya asafune’ koma Mutharika mpaka 2024.

“Wathu ndi APM amene timutengere kuchisankho cha 2019. Kaya ena afuna kaya ayi koma zichitika motero,” adatero Jeffrey.

Mbali inayi, phungu wa chipanicho kummawa kwa boma la Mulanje, Bon Kalindo adati kaya wina afune kaya asafune, chipanichi chitsogozedwa ndi Chilima.

Iye adati zomwe akupanga akuluakulu ena a DPP kuli ngati ‘kuwaonjezera mafuta’ kuti ganizo lawo lobweretsa Chilima litheke.

“APM ayi, wakula. Kodi atitsogolere kuti? koma n’chifukwa chiyani tikufuna kuti okalamba azititsogolera? Atitsogolere kuti? Tilipo gulu, tikukumana ndipo posakhalitsa tidziwitsa Amalawi zomwe takonza,” adatero Kalindo.

Iye adati vuto lalikulu ndi anthu amene azinga Mutharika. Izi zikupherezera zomwe adanena mkazi wa mtsogoleri wakale wa dziko lino Callista Mutharika, ayemwe adashosha mavu m’khomola pobwera poyera kunena kuti mlamu wake Peter akukakamizidwa kudzaimanso ndi ‘zilombo’ zimene zamuzungulira.

“APM ndi munthu wabwino koma wazunguliridwa ndi ng’ona. Ndipo ngati sasamala zimudya….komwe kuli Bingu [wa Mutharika] adziwe kuti anthu amene adasangalala pa imfa yawo azungulira mbale wake ndipo tsiku lililonse amukhzadzulirana,” adatero iye.

Mkulu woyang’anira achinyamata m’chipanicho Louis Ngalande adati nkhaniyi kuti itheretu pafunika kuti DPP ichtitse msonkhano waukulu komwe akasankhe mtsogoleri.

Ngalande amene achinyamata ena m’chipanicho amupempha kuti atule pansi udindo wake posankha Chilima wati sakubwerera m’mbuyo mpaka ganizo lake litatheka.

Izi zikuchitika kutsatira moto womwe adayatsa Callista Mutharika, mkazi wa Bingu wofuna Chilima adzaime osati mlamu wake amene akuti wakalamba.

Related Articles

Back to top button