Nkhani

Makuponi n’chipsinjo—Mafumu

Kuchepa kwa makuponi ogulira zipangizo za ulimi zotsika mtengo omwe boma limagawa kwa anthu mogwirizana ndi mafumu, kukubweretsa chitonzo kwa mafumuwo ndi maudani osatha mmidzi.

Izi zikudzanso makamaka pamene boma latsitsa chiwerengero cha opindula pa chilinganizochi kuchoka pa 1.5 miliyoni kufika pa 900 000.

Mwanamvekha kuyendera makuponi pomwe amafika kubwalo la ndege la Chileka

Mafumu ena ati chiwerengero cha makuponi omwe amaperekedwa chimangobweretsa mavuto mmalo mothetsa umphawi ngati mmene cholinga cha pologalamuyi chimanenera.

Mwachitsanzo, T/A Maseya wa ku Chikwawa limodzi mwa madera omwe akuti makuponi ayamba kale kugawidwa, wati mmudzi mwa Gulupu Tome momwe muli mabanja oposa 70, angolandira makuponi 6 okha chaka chino.

“Chimenechi chakhala chizolowezi, moti anthu amadana ndi mafumu awo pomaona ngati mafumuwo akubisa makuponi. A gulupu a Tome adabwera kudzandidandaulira kuti zinthu zavuta m’dera lawo,” adatero Maseya.

Iye adati zikafika apa, anthu nawo amayamba kunyanyala kutenga nawo gawo pankhani za chitukuko pomati omwe adalandira makuponi ndiwo akagwire ntchitozo zinthu nkumatsalira mafumu.

Senior Chief Chadza wa ku Lilongwe komwe akuti makuponi sadafike adati nkhani ndi ya maudani yomweyo ndipo adapereka chitsanzo choti dera la Gulupu Mnongwa lomwe lili ndi mabanja 170, chaka chatha adalandira makuponi 19 okha.

“Mabanja ambiri sadalandire makuponi ndipo zidali zovuta kwambiri moti pano tingoyembekezera kuti makuponiwo akafika kaya kukhala zotani chifukwa anthu adabzala kale m’mitima yawo kuti mafumu amabisa makuponi pomwe si choncho,” adatero Chadza.

Mfumuyo idati ikuona kuti boma likadapereka mphamvu zonse zopanga mapulani akagawidwe ku makhonsolo mwina bwenzi zinthu zikuyenda koma kuchuluka kwa makuponi opita kwa mafumu amakonzedwa kulikulu la boma.

Ngakhale zili choncho, mfumuyo idati anthu ake ali kalikiliki kukonzekera ulimi chifukwa ambiri mwa iwo adazolowera kuti asamadalire pulogalamu ya sabuside kuopa kugwiritsidwa fuwa la moto.

M’madera a kumpoto nako akuti makuponiwa sadayambe kufika ndipo T/A Khonsolo wa ku Mzimba wati izi zachititsa kuti anthu ayambe kukonzekera ulimi chifukwa sakudziwa pomwe makuponi adzafike.

“Tili ndi midzi ikuluikulu kwambiri koma nzomvetsa chisoni kuti chiwerengero cha makuponi chomwe timalandira moti zimangothera m’maudani osasimbika pakati pa anthu ndi mafumu komanso anthu okhaokha,” adatero Khonsolo.

Pulezidenti wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Alfred Kapichira Banda adati pulogalamu ya sabuside imalozera tsogolola ntchito za malimidwe choncho n’koyenera kuitenga bwino.

Iye adati boma likuyenera kuunika bwino nkhani ya chiwerengero cha makuponi omwe limapereka pa mfumu iliyonse komanso kuunika nthawi yomwe makuponi amabwerera ndi nyengo yomwe zipangizo zimapezekera.

“Tiyamike kuti chaka chino zikuoneka ngati zayenda msanga koma tipemphe kuti chimenechi chikhale chizolowezi chifukwa alimi amamangika pa ntchito yawo chifukwa chosadziwa za tsogolo la sabuside,” adatero Kapichira Banda.

Chaka chino monga zidalili chaka chatha, anthu 900 000 ndiwo akuyembekezeka kupindula pa pulogalamu ya sabuside ndipo nduna ya zamalimidwe, mthilira ndi chitukuko cha madzi Joseph Mwanamvekha adalengeza kuti makuponi onse adafika kale m’dziko muno.

Ndunayi idatsegulira ntchito yogawa makuponi Lachitatu sabata yatha m’boma la Mchinji komwe idachenjeza makampani ogulitsa zipangizo za sabuside, mafumu ndi akuluakulu ena kuti asayerekeze kulowetsapo zachinyengo.

Pakadalipano, bwalo la milandu mumzinda wa Blantyre laimitsa kaye ntchito zonse zokhudzana ndi makuponi, concho unduna wa malimidwe ndi bungwe la alimi aang’ono la Smallholder Farmers Revolving Fund of Malawi (SFFRFM) sapitiriza ntchito yogawa makuponi pomwe makampani amene akutumiza feteleza kumadera asapitirize ntchitoyo. Izi zidadza kampani ya Transglobe imene idachotsedwa pamndandanda wa makampani wopititsa feteleza kumidzi.

Wapampando wa komiti ya zamalimidwe m’Nyumba ya Malamulo Joseph Chidanti Malunga adati n’zokondweretsanso kuti chaka chino makuponi afika nthawi yabwino poyerekeza ndi chaka chatha pomwe makuponi amafika mpaka mu December madera ena asadalandire ndipo pomwe amalandira nkuti chimanga chitafula. n

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button