Nkhani

Malamulo a ukwati akutsutsana

Listen to this article

Kutanthauzira lamulo lokhudza maukwati a ana kukhala kovuta tsopano pamene pali kusemphana pakati pa zomwe zidalembedwa m’malamulo oyendetsera adziko lino ndi zomwe zili m’malamulo okhudza mabanja la Divorce and Relations Act.

Gawo 22 ndime 6 ya malamulo a dziko lino limati palibe munthu woposa zaka 18 adzaletsedwe kukwatira kapena kukwatiwa. Ndime 7 imati munthu wa zaka pakati pa 15 ndi 18 angathe kukwatiwa kapena kukwatira ngati patakhala chilolezo kuchoka kwa makolo kapena womuyang’anira.Family_

Izi zikusemphana ndi zomwe zili mu lamulo latsopano loyendetsera maukwati zoletsa ukwati wa munthu wosaposa zaka 18.

Ku Dedza, T/A Kachindamoto akuchotsa mafumu amene apezeka akuvomereza ukwati wa mwana wosaposa zaka 18.

Mwa chitsanzo nyakwawa Galuanenenji idachotsedwa pampando chifukwa chovomereza ukwati wa mtsikana wa zaka 15 ngakhale makolo ake adavomereza kuti ukwatiwo uchitike.

Kachindamoto akuti mphamvu akuzitenga mu malamulo oyendetsera maukwati momwe akuletsa ukwati wa mwana wosaposa zaka 18. “Tsono kuti tichotse mfumu pampando, malamulo amenewa tidachita kugwirizana tokha kuno ndiye mfumu yomwe yalakwitsa ikuchotsedwa ndipo mafumu anayi achotsedwa,” adatero Kachindamoto.

Koma Esmie Tembenu wa Blantyre Child Justice Magistrate akuti pali kusokonekera kwazinthu chifukwa cha Divorce and Relations Act.

“Chifukwa cha ubwino woti ana kuti azipita kusukulu, lamulo la maukwati ndi lomwe tikugwiritsa ntchito komabe tili ndi mantha chifukwa izi si zomwe zili m’malamulo adziko lino.

“Ngati wina atakutengera kubwalo la milandu, angathe kukapambana mlandu chifukwa malamulo adziko lino okha ndiwo ali ndi mphamvu,” adatero Tembenu.

Naye mphunzitsi wa za malamulo kusukulu ya Chancellor College Edge Kanyongolo akuti pamenepa pali kusokonekera kwa zinthu komabe wati lamulo la dziko lino ndilo lili ndi mphamvu.

Masiku apitawa, Kanyongolo adati pofuna kugwiritsa zomwe zili mu lamuloli, ndiye pakuyenera kukonza gawo 22 lomwe lili m’malamulo adziko lino.

“Ngakhalenso kukonza malamulowo nkovuta chifukwa pakuyenera pachitike lifalendamu kuti lamuloli likonzedwe,” adatero Kanyongolo. n

Related Articles

Back to top button
Translate »