Nkhani

Malawi ipunthanandi Zimbabwe lero

Listen to this article

 

Mpikisano wa matimu a mu Africa wa Africa Cup of Nations (Afcon) wayamba lero pamene matimu osiyanasiyana akuthethetsana.

Matimu a m’gulu L, momwe muli Malawi, Zimbabwe, Swaziland ndi Guinea, ayambanso kutuwitsana lero pamene Malawi ikulandira Zimbabwe pa Kamuzu Stadium masanawa.Flames-vs-Zimbabwe-2

Zimbabwe, yomwe ili panambala 119 m’dziko lapansi pamomwe matimu akuchitira pamndandanda wa Fifa, yakumana ndi zokhoma zosowa ndalama ndipo izi zidachititsa kuti timuyi itulutse mochedwa maina a osewera amene akubwera ku Malawi kuno.

Lachiwiri usiku, kochi wa timuyi, Kalisto Pasuwa, adatulutsa mndandanda wa osewera 19 kuti abwere kudzazimitsa Flames.

Malinga ndi nyuzipepala ya TheHerald ya ku Zimbabweko, timuyi idayamba zokonzekera zake Lachitatu koma ndalama zoti igwiritsire ntchito kubwera ku Malawi zidali zisadapezeke.

Koma kumbali ya Malawi, zonse zili m’chimake, malinga ndi kochi Young Chimodzi.

“Tidakasewera ndi Egypt, ngakhale tidagonja [2-1] komabe zatithandiza kuti tione anyamata amene tingawagwiritsire ntchito pamene tikumane ndi Zimbabwe. Tingathe kunena kuti chilichonse chatheka,” adatero Chimodzi, amene timu yake yakhala m’kampu kwa mwezi tsopano.

Timuyi ili ndi osewera onse amene adakasewera nawo ku South Africa mumpikisano wa Cosafa komanso akatswiri ena amene amasewera m’maiko ena.

Ku Egypt, John Banda ndiye adagoletsa chigoli cha Malawi. Lero maso akhale pa katswiriyu komanso Atusaye Nyondo ndi Esau Kanyenda kutsogolo kwa Malawi.

Zimbabwe yaitana Nyasha Mushekwi amene amasewera ku Sweden. Mnyamatayu watchuka ndi kumwetsa zigoli kumeneko ndipo masanawa Flames iyenera kuchenjera naye ameneyu.

Masewero omaliza pakati pa matimuwa amene adachitikiranso pabwalo lomweli pa 5 March chaka chatha, Malawi idagonja 1-4 ndipo Atusaye ndiye adachinya chigoli cha Malawi.

Related Articles

Back to top button