Chichewa

Maliro akapeza ukwati

Listen to this article

 

Pamoyo wa munthu, mavuto kapena mtendere zimabwera mosayembekezera. Nthawi zina zovuta zimagwa pamene pali zilinganizo zina zachimwemwe monga ukwati. GIFT CHIMULU adacheza ndi gogochalo Pemba a m’boma la Salima kuti amve zambiri maliro akapeza ukwati pa mudzi zimatani? Adacheza motere:

Gogo zimatani kudera kwanu kuno maliro akagwa pabanja lomwe lakonza chilinganizo cha ukwati?

Choyamba ndinene kuti ngati zikafika potero, mafumu ndi mikoko yogona imaima mitu chifukwa cha nkhani imeneyi. Koma ndinene kuti zimatengera kwambiri kuti kodi ubale wa amene wapitayo ndi amene akupanga ukwati ndi wotani?

Pemba kufotokozera Chimulu momwe zimakhalira

Tiunikireni tsopano zikatero ngati gogochalo, gawo lanu limakhala lotani?

Monga mudziwa mafumu amakhala ndi mbali yaikulu panthawi ya ukwati angakhalenso maliro, koma zotero zikagwa timayenerabe kukumana ndi a kubanja pa ganizo lawo, koma nditsindike kuti nthawi zambiri timatsekera kaye zovutazo ndi cholinga choti mwambo waukwati udutsepo.

 

Koma zikatero ena sanganene kuti mwapeputsa maliro?

Maganizo otere atha kukhalapo koma choti ndikuuzeni nchoti kukonzekera ukwati sikwatsiku limodzi ayi, pamene maliro amangodza mwadzidzidzi. Komanso timakhulupirira kuti pamene wina wamwalira zake zimakhala kuti zatha, choncho amoyo sangaimike zichitochito zawo kaamba ka zovuta.

 

Inu gogo pa nthawi yanu ngati mfumu zinakugweraponi zoterezi?

Pa nthawi yanga ayi! sizidandionekerepo koma ndaziona zikuchika ndili wamng’ono maliro adayamba atsekeredwa kaye kudikira ukwati udutsepo. Zonse zidayenda bwinobwino popanda milandu potsatira chilinganizo chotero.

 

Koma miyambo ngati imeneyi ana a masiku ano sakuyidziwatu sadzatitukwana tsiku lina tikadzatsekera maliro kaamba ka ukwati?

Nkhawa yanu ndi yoona ndipo zikufunikiradi dongosolo kuti ana ongobadwa kumenewa azidziwa miyambo ya makolo komanso momwe angathanirane ndi mavuto okhudza miyambo komanso zikhalidwe zawo. Ndipo gawo lalikulu lili m’manja mwa makolo awo kuti aziwaunikira ana awo.

 

Pomaliza gogo mzimu wa wotisiyayo mukuona ngati amaganiza zotani pomwe tasiya mwambo woika m’manda thupi kaamba ka ukwati?

Mukuganiza kwambiri koma monga ndafotokozera muja zoterezi zimachitika mosapanganika, ndipo ngati mzimu wake wakwiya mapemphero amachotsa zonsezo. Ndimalize ndi kunena kuti ngakhale izi zili choncho nthawi zones maliro timawapatsa ulemu wofunikira, timatha kuimika zina zonse kaamba ka zina ndi zina koma paukwati pokhapo ziyenera kutero basi.

Mwatero gogo?

Eya anthu akavine kenako kulira komanso mwambo wonse wa maliro pambuyo.

Related Articles

Back to top button