Chichewa

Zipolowe ku mapulaimale

chotsutsa cha MCP chidaimitsa mapulaimale ake kaamba ka zipolowe ku Dedza, zipani zandale, kuphatikizapo MCP, zatsindika kuti zichilimika kuti zipolowe ku mapulaimale zisachitike.

Magazi adachucha ku mapulaimale a MCP kudera la kumpoto kwa bomalo Lachiwiri lapitalo potsatira mkwiyo wa masapota. Mwazi ukukha, katundu adaonongedwa ndi anthu amene ankagenda poyesetsa kusokoneza kuti mapulaimalewo asachitike poganiza kuti pankachitika zachinyengo. Ena adavulala pa chipwilikiticho.

Koma mneneri wa MCP, mbusa Maurice Munthali watui zipolowezo zidali zomvetsa chisoni ndipo chipanicho chiyambanso mapulaimalewa kuyambira Lachisanu likudzali chifukwa akonza zovuta zonse.

Kaliati: Kulibe
kudzimbuka

“Mavuto analipo onse atha ndipo tikuuza makandideti onse a m’madera 191 amene atsalira kuti zipolowe ndi zosafunika ku mapulaimale. Ndondomeko zathu zikupatsa anthu a kudera kusonkha amene akuwafuna ndipo akuluakulu a kuchipani azikangoonerera kuti zonse ziyende bwino,” adatero Munthali.

Zipolowe zidayamba ku mapulaimalewo pomwe Savel Kafwafwa, yemwe amapikisana ndi phungu waderalo Patrick Chilongola adati saimanso pachisankhocho chifukwa amafuna kuberedwa. Anthu ena adayamba kugenda kuti chisankhocho chime ndipo ena adaswa galimoto ndi nyumba ya Chilongola.

Koma Chilondola wati ichi chidali chiwembu chabe chofuna kusokoneza chifukwa padalibe malingaliro aliwonse obera mapulaimalewo.

“Anthu ondifunira zabwino adali atandichenjeza kale kuti andikonzekera chifukwa amadziwa kuti sangandigwetse ndi votisi,” watero Chilondola.

Pomwe MCP ikuti yasokerera mabowo omwe analipo, mneneri wa chipani cha UDF Ken Ndanga wati chipanicho sichidzatsata njira yoti ofuna munthu azikaima kumbuyo kwake, zimene wati zimadzetsa zipolowe komanso kuti chisankho chisayende mwa chilungamo.

“Zoima kumbuyo kwa kandideti zimachititsa kuti ovota asamasuke. Ndipo ena akangoona kuti kumbuyo kwawo kuli anthu ochepa, amatsutsa zotsatira za chisankho tisanawerenge n’komwe. Mapeto ake zikhonza kukhala ziwawa,” adatero Ndanga.

Mlembi wamkulu wa United Transformation Movement (UTM) Patricia Kaliati adati chipanichi chidayamba kale kukambirana ndi onse ofuna kudzapikisana nawo kuti akadzagwa asadzadzimbuke ndipo zokambiranazo zikubala zipatso.

“Ena takumana nawo kale ndipo amvetsetsa n’kutitsimikizira kuti akadzagwa, sadzadzimbuka koma adzagwira ntchito ndi omwe adzapambane kuti mphamvu zidzachuluke,” adatero Kaliati.

Mlembi wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) Grezelder Jeffrey adati chipanicho chidayamba kale kukambirana ndi ofuna maudindo kuti adzavomereze zotsatira za mapulaimale.

“Mbali imeneyo takonza kale ndipo tili ndi chikhulupiliro kuti sipadzakhala zodzimbuka zilizonse chifukwa taunikirana nawo onse ofuna maudindo ndipo amvetsetsa,” adatero Jeffrey.

Akatswiri pa zandale George Phiri wa ku University of Livingstonia ndi Mustafa Hussein wa ku Chancellor College adati zipani zikuyenera kusamala pochita mapulaimale kuopa zipolowe monga zidalili ku Dedza.

Phiri wati zipolowem’chipani si zabwino makamaka panthawi ino pomwe zipani zili kalikiliki kubzala chikhulupiliro cha utsogoleri wabwino mwa anthu.

“Mukaonetsetsa, nkhawa zambiri zomwe anthu ali nazo pautsogoleri ndi mtendere ndi ulamuliro wa demokalase yeniyeni ndiye zipani zikuyenera kuphathirira pa nkhawa zimenezi. Mkangano ngati wa ku Dedza ukhonza kupeweka ngati atsogoleri atsata mfundo za chilungamo,” adatero Phiri.

Ndipo Hussein wati atsogoleri a zipani akuyenera kupanga ndondomeko zoti mavuto a m’zipani achepe kuopa kugwetsa mphwayi anthu.

“Iyi si nthawi yopanga zachibwana chifukwa masiku apita kale. Chofunika apa n’kupanga njira zopewa mavuto m’chipani. Zipani zones zidziwe izi pomwe mapulaimale angoyamba kumene,” watero Hussein.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button