Achinyamata akambirana za m’manifesto

 

Nthambi ya achinyamata ya chipani cha Malawi Congress Party (MCP) yakambirana mfundo zokhudza achinyamata zomwe chipani chawo chiyike m’manifesto yake yokopera anthu pachisankho chikudzachi.

Woyang’anira za achinyamata Richard Chimwendo Banda watsimikiza izi ndipo mneneri wachipanichi mbusa Maurice Munthali wati kupatula achinyamatawa, chipanichi chikulandira maganizo kuchokera ku magulu osiyanasiyana.

Ena mwa achinyamata amene adafika kumsonkhanowo

“Tili mkati mopanga manifesto yathu poonjezera zomwe tidaiwala mu 2014. Imodzi mwa nthambi zomwe taikapo mtima kwambiri ndi achinyamata tsono tidaona kuti n’kwabwino akambirane okha mfundo zowakhudza n’kutipatsa,” watero Munthali.

Achinyamata a MCP a m’chigawo chapakati ndi nthumwi za m’zigawo zina amakumana kulikulu la chipanichi pa 23 ndi 24 August mumzinda wa Lilongwe kukambirana mfundozo ndipo Chimwendo Banda wati msonkhano ngati omwewu ukachitikaso m’zigawo zina.

“Pamsonkhanowu, tidali ndi achinyamata 1 000 ochokera m’madera onse oyimiliridwa ndi aphungu m’chigawo chapakati ndi mphepepete mwanyanja komanso nthumwi za m’makomiti a m’zigawo. Misonkhano ngati yomweyi ikachitikanso m’zigawo zina,” adatero iye.

Iye adati kumsonkhanoko, achinyamata adatulutsa nkhani zambiri zowakhudza n’kuzikambirana ndipo adamanga mfundo za momwe akuonera kuti nkhanizi zikhonza kukonzedwa ndi atsogoleri.

Iye wati chipanichi chidachita izi ngati njira imodzi yoperekera mphamvu kwa achinyamata kupanga ziganizo za momwe dziko lingayendere bwino ndipo wati ali n’chikhulupiriro kuti atsogoleri a chipanichi akhutitsidwa ndi mfundozo.

Pothirirapo ndemanga, Munthali adati komiti yaikulu idasangalala koposa ndi momwe msonkhano wa achinyamatawo udayendera komanso mfundo zomwe adamanga n’kupereka ku likulu.

“Mfundo zomwe adatipatsa zikusonyeza kuti m’chipanimu tili ndi achinyamata akupsa m’maganizo omwe angathandizedi pachitukuko cha dziko. Mfundo zawo tazitenga ndipo tiziphatikiza m’manifesto yathu chifukwa n’zokomera achimata onse m’dziko muno,” watero Munthali.

Woyendetsa gulu la mphala ya achinyamata la Youth Consultative Forum Edward Chileka Banda wayamikira zomwe chipani cha MCP chapanga ndipo wati zingakhale bwino zipani zonse zitatengera mchitidwewu.

“Zimenezi n’zomwe timafuna ngati achinyamata kupatsidwa mphamvu osati kumangogwiritsidwa ntchito ngati osapota chipani kapena zida za zipolowe ndi andale ayi. Uku ndiye kuphunzitsa achinyamata utsogoleri,” watero Chileka Banda.

Iye wati kupatula momwe chipani cha MCP chapangira, mpofunikaso kuti achinyamata azipatsidwa mpata wokwanira ogwira ntchito zogwirizana ndi maluso awo osati kumangowaponderedza.

Share This Post

One Comment - Write a Comment

Comments are closed.

Powered by