Nkhani

Mavuto okhaokha m’ndondomeko ya AIP

Listen to this article

Mavuto amanga nthenje m’pulogalamu ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo ya AIP ngakhale kuti nduna ya zaulimi a Sam Kawale adalonjeza kuti ndondomeko ya chaka chino yasefa mavuto omwe adalipo chaka chatha.

M’pulogalamuyi chaka chatha mudali mavuto monga katangale, kuvuta kwa netiweki, zipangizo zina osapezeka kumsika komanso alimi kugonera masiku kumsika kudikira kuti mwayi ogula zipangizo uwagwere.

Kugula zipangizo za AIP kwadza ndi mavuto ake

Polengeza za kutheka kwa pulogalamu ya AIP ya 2022 m’Nyumba ya Malamulo pamkumano omwe watha dzulo, a Kawale adalonjeza kuti mavuto ngati amenewa achepa kapena saonekeratu chaka chino chifukwa cha ndondomeko yomwe yakhazikitsidwa.

Koma kauniuni wa Tamvani wapeza kuti lonjezolo laphwanyika chifukwa alimi ambiri akudandaulabe zogonera kumsika kufuna kugula zipangizo komanso kuti mwayi ukapezeka, akuumilizidwa kupereka kangachepe kuti agule.

Kauniuni yemwe adachitika kumayambiliro kwa December m’zigawo zonse adapeza kuti alimi akupereka K5 000 yapamwamba kuti agule fetereza kutanthauza kuti akupereka K35 000 pa matumba awiri mmalo mwa K30 000.

Alimi ena adaulula kuti akugonera kumsika chifukwa nthawi zambiri akapita, netiweki ikukhala kulibe kapena zipangizozo sizikupezeka mokwanira zomwe zikuwasokonezera ntchito zina za kumunda ndi pakhomo.

A Jessie Kananji a kwa Kachere ku Blantyre adati iwo adagonera masiku awiri kumsika kudikilira kuti agule zipangizo zaulimi zomwe akapeza mwayi ogula akuyenera kusunga K5 000 yodyetsera ogulitsa zipangizozo.

“Anthu tavutika kale kusaka ndalama kuti tipeze zipangizo zaulimi kenako tilowenso ntchito yogonera kumsika. Ukapezanso mwayi woti ugulewo, ukuyenera kuti ukhale ndi K5 000 yodyetsera? Ambiritu tikupilira kugona ndi njala kuno kuopa kuwononga yogulira zipangizozo tikadya,” adatero a Kananji.

Madandaulo ngati omwewa adapezekanso m’madera ena m’zigawo zonse koma mneneri wa unduna wa zaulimi a Geoffrey Banda adati unduna ukukonza zovuta zomwe zinkapangitsa mavutowo monga a netiweki ndi kusapezeka kwa zipangizo.

“Tikukonza mavuto onsewo moti alimi ayembekezere kuti zinthu zisintha posachedwa ndipo saonanso mavuto kupita chitsogolo. Koma chomwe alimi asadandaule kwambiri nchoti fetereza alipo okwanira wa aliyense yemwe akuyenera kupindula,” adatero a Banda.

Iwo adati undunawo ukukozanso za mavuto a netiweki omwe akumaoneka nthawi zomwe alimi akufuna kugula zipangizo ndipo izi zimapachititsa alimiwo kudikilira mpaka pomwe netiweki iyambe kugwira.

Koma Tamvani atazunguliranso m’madera ena makamaka m’chigawo chapakati m’sabatayi adapeza kuti alimi akudandaulabe za mavuto a netiweki, kukhalitsa kumsika ndi kukakamizidwa kuti azidyetsera akafuna kugula zipangizo.

A Joram Masiye a ku Salima ati iwo adatuma mnyamata kukagula fetereza wa AIP kumsika Lachiwiri koma adabwerera chifukwa cha netiweki koma mnyamatayo pobwerera adakumana ndi anthu ena omwe adamuuza kuti azingobwerera ngati alibe yodyetsera.

“Apa zidandipatsa maganizo woti mwina nkhani ya netiwekiyo ndi yabodza koma mwina ogulitsawo akufuna chinyengo kuti munthu agule ndiye zikupereka mantha kuti alimi ambiri sakwanitsa,” adatero a Masiye.

Koma a Banda sadayankhepo kanthu pankhaniyo ndipo adauza Tamvani kuti samatsata za kuofesi chifukwa adali kwina kokagwira ntchito.

“Pamenepo ndilibe lipoti lililonse lokhudza za AIP chifukwa ndakhala nthawi osapita kuofesi, mwina ndifufuze kaye,” adatero a Banda.

Koma mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) a Manesi Nkhata adati vuto lalikulu ndi loti boma likugwiritsa ntchito bungwe limodzi lokha la SFFRFM m’pulogalamu ya AIP.

Iwo ati njirayi yachepetsa misika yogulirako zipangizo zaulimi kotero alimi akukanganirana zipangizozo zikafika.

“Pulogalamuyi yakumana ndi zovuta zambiri kuchoka kumayambiliro ndiye boma limafunika kuyesetsa kuti mavuto amenewa athe. Mwachitsanzo, akufunika kuonjezera misika chifukwa padakalipano, makampani sakugulitsa nawo zipangizo ngati fetereza,” atero a Nkhata.

Koma ngakhale zikuvuta choncho kwina ndi kwina, Tamvani adapeza zipangizo zitafika m’madera ena monga kwa Kamwanya ku Mchinji, kwa Msundwe ku Lilongwe ndi ku Mphomwa ku Kasungu.

A Kawale adati onse omwe apezeke ndi mlandu okhudzana ndi pulogalamu ya AIP adzaweruzidwa moyenera chifukwa undunawo ukugwira ntchito ndi maunduna ena kuphatikizapo apolisi ndi a Malawi Bureau of Standards.

Related Articles

Back to top button