Nkhani

MCP, UTM asainira mgwirizano

Kudali khwimbi la anthu ku Kamuzu Institute for Sports ku Lilongwe Lachinayi pomwe zipani zotsutsa zimasayinira mgwirizano wawo motsogozedwa ndi Lazarus Chakwera wa Malawi Congress Party (MCP) ndi Saulos Chilima wa UTM Party.

Mumgwirizanowu muli zipani za MCP, UTM Party, People’s Party, Aford, Mafunde, Umodzi Party, Petra, Freedom Party ndi PPM.

Chakwera ndi Chilima kupatsana moni

Kadaulo pa ndale George Phiri wati mgwirizano wangati umenewu sudachitikeponso m’dziko la Malawi ndipo iye adati zipanizi zikapitirira kuyenda limodzi chonchi, palibe chokaikitsa kuti adzapambana pachisankho chobwereza chomwe chikubwera mtsogolomu.

“Mukakumbuka, ndidanenapo mmbuyomo chisadachitike chisankho cha pa 21 May 2019 kuti mgwirizano wa zipani za MCP ndi UTM ndiwoopsa ndiye pano tikunena za zipani zingapo, amenewo simasewera,” adatero Phiri.

Padakalipano, minofu ya mgwirizanowo ikadali yobisika ndipo yemwe adayendetsa mwambowo Richard Chimwendo Banda adati pakhala tsiku lapadera lomwe zipanizo zidzalengeze momwe maudindo akhalire mumgwirizanowo.

Mgwirizanowo adasayinira ndi Chakwera ndi Chilima komanso alembi a zipanizo Eisenhower Mkaka ndi Patricia Kaliati ndipo mtsogoleri wakale wadziko lino Joyce Banda adasayina ngati mboni ya MCP pomwe Enoch Chihana wa Aford adasayina ngati mboni ya UTM Party.

Chakwera ndi Chilima onse polankhula kwa khwimbiro adati tsiku losayinirana mgwirizanowo lidali potembenukira pa dziko la Malawi kuchoka m’mavuto adzawoneni n’kuyamba kulunjika ku dziko la mkaka ndi uchi.

Chilima yemwe adayamba kulankhula adati ulendo omwe mgwirizanowo udayamba ndi wopita ku nyumba ya boma kuti akayendetse dziko mwangwiro.

“Ulendo wathuwu tikulowera kunyumba ya boma. Mmodzi mwa ife akakhala kumeneko chifukwa ulendo uno palibe zoti wina abera chisankho. Tamva kale kuti akuyesayesa njira zoti akoke mphamvu za mafoni kuti azikazisokonezera ku nyumba imene ija pachisankho,” adatero Chilima akuloza nyumba ya boma ya ku Lilongwe.

Chakwera adatsimikizira anthu kuti nthawi yotenga boma yakwana ndipo adawalimbikitsa kuti asadandaule chilichonse.

Iye adadzudzula zomwe adapanga mtsogoleri wadziko lino Peter Mutharika pokana kusayina mabilu oyendetsera chisankho komanso kunyazitsa komiti yoona zosankha anthu m’maudindo ena m’boma (PAC) pokana kuchotsa makomishona a MEC.

“Chavuta apa n’kufunitsitsa kudzikundikira mphamvu ngakhale mphamvuzo zikuwakana. Chomwe timadziwa ife n’choti mphamvu ndi za wanthu ife atsogoleri ndi wongotumikira,” adatero Chakwera.

Iye adatenga kanthawi kuphunzitsa anthuwo za matenda a coronavirus.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button