Nkhani

Mfumukazi ichereza mayi wobereka ana 5 pa kamodzi

Listen to this article

Mkazi wa Inkosi ya Makhosi Gomani V, Inkosikati Rishaladza Khanyisa Gomani wati kuchuluka kwa mimba za ana achichepere kukukolezera kusachita bwino kwa ana asukulu pamayeso a Maneb m’bomali.

A Gomani adanena izi pomwe adatsagana ndi mlangizi wa boma pa nkhani za uchembere wabwino mayi Dorothy Ngoma kukayendera mayi wina wa zaka 29 Ledina Paul yemwe anabereka ana asanu pa chipatala cha m’boma la Ntcheu.

Inkosikati kuchereza amayi m’chikuta cha pachipatalapo

Iwo anati mwachitsanzo, zotsatira za mayeso a boma zaka zapitazi, boma la Ntcheu lakhala likupezeka kumapeto kwenikweni kwa maboma omwe sanachite bwino pa mayesowa.

“Mimba zomwe atsikana akumatenga zikukolezera kwambiri mchitidwe osiira sukulu panjira popeza atsikanawa tsopano akumaika chidwi chawo posamala makanda omwe abereka zomwe zikumasokonezanso ngakhale zotsatsatira za mayeso zikatuluka,” anadandaula motero.

Iwo adapempha atsikana omwe anasiyira sukulu panjira kaamba ka uchembere kuti abwerere kukayambanso sukulu komanso n’kuwalimbikitsa kugwiritsa ntchito njira zakulera kufikira pomwe adzafike podziimila paokha ndinso kukhala ndi banja lokhazikika.

Ndipo mlangizi wa boma pa nkhani zauchembere wabwino mayi Ngoma adati ndi wokhudzika kwambiri kaamba ka kuchuluka kwa atsikana omwe chiwerengero chawo chikukwera m’zipatala m’dziko muno.

“Ndi zomvetsa chisoni kuona ana a zaka 12 akupezeka m’zipinda zoberekeramo komwe sakuyenera kupezeka. Izi zikudzetsa kuchulukana m’zipindazi, sitili okonzeka ngati dziko kukhala ndi ana ochuluka chonchi m’zipatalamo chifukwa tikupatsa ntchito yaikulu kwambiri kwa anzathu omwe amagwira ntchito m’zipatalamu,” adatero iwo.

A Ngoma adalangiza achinyamata kuti apewe mchitidwe wogonana ali achichepere ndipo kuti m’malo mwake aike chidwi kwambiri pa maphunziro kuti adzakhale nzika zodalilika.

“Mwachitsanzo, amai achicheperewa ukawapeza m’zipatalamu atabereka, amachita kuoneka kuti alibe zodziyenereza kulera anawa kumbali ya chuma komanso thandizo lina. Izi zikuthandiza kukolezeranso umphawi mdziko kuno,” adaonjeza motero.

Mkulu wa anamwino pa chipatala cha Ntcheu mayi Gloria Magombo adavomereza zoti m’zipatala za m’bomalo akulandira ana ochuluka omwe amapita kukachira m’zipatalazi zomwe ati ilinso lakhala vuto lalikulu poti atsikana achichepere amakhala paziopsezo zazikulu pobereka.

“Tikukhaladi ndi chiwerengero chochuluka cha amai omwe ukumabwera kudzabereka. Ena mwaiwo ndi achichepere moti patsiku timachiza amai oposa 24 koma nthawi zina pachipatala pokhapano timathanso kubadwitsa ana mpaka 30 pa tsiku limodzi,” adatero iwo.

Related Articles

Back to top button
Translate »