Nkhani

Msungwana adakokera boma kukhoti

Listen to this article

Chaka cha 2023 chikupita ndi nkhani zake, imodzi mwa nkhani zimene zidayala nthenje ndi ya msungwana wa zaka 14 yemwe amaimba sukulu mu sitandade 5 atakamang’ala kukhoti kuti limasulire bwino zifukwa zomwe amayi angaloledwe kuchotsa pakati.

Izi zidadza pomwe mabungwe ena akumenyera kuti lamulo lochotsa mimba lisinthidwe mogwirizana ndi zimene idapeza komishoni yosakatula malamulo a dziko lino ya Law Commission.

Bungwelo lidati lamulolo lisinthidwe kuti aonjezere zifukwa zimene amayi angachotsere mimba kupatula zoti kuchotsa mimbako kuchitike ngati ingaike pachiopsezo umoyo wa amayi. Iyo idati lamulolo lionjezere kuti amayi angachotse mimba ngati mayi anapatsidwa mimba atagwiriridwa kapena kupatsidwa ndi mbale wake.

Msungwana adakamang’alayo adagwiriridwa ndi njonda ina yomwe pano ikuseweza zaka 14 kundende koma akuti atapita kuchipatala kuti akamuthandize kuchotsa mimba yomwe idabwera kaamba kogwiriridwako koma achipatalawo adakana pempholo.

Malingana ndi kafukufuku yemwe adachita akadaulo kusukulu ya ukachenjede wa za umoyo ya Kamuzu University of Health Sciences (Kuhes) wokhudza asungwana omwe sadafike zaka 18 ndipo adatenga mimba kaamba kogwiriridwa moyo wawo umakhala pa chiopsezo.

“Ambiri mwa asungwana omwe adatenga mbali pa kafukufukuyo adati amaona ngati moyo wawo wasokonekera moti amalingalira zongodzipha poona kuti tsogolo lawo laonongeka,” zikutero zotsatira za kafukufukuyo.

Mabungwe a Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), Nyale Institute, Young Women’s Consortium (YWC), Centre for Reproductive Rights (CRR) ndi Afyana Haki ati athandiza msungwanayo mpaka pomwe khoti lidzagamule nkhani yake.

Mkulu wa bungwe la CHRR a Michael Kaiyatsa ati nkhaniyi siyikukhudza mtsutso womwe ulipo kale woti malamulo azilola amayi ndi asungwana kuchotsa mimba ngati afuna kutero.

“Tikudziwa kuti pali kale mtsutso wokhudza kuchotsa mimba, nkhani ya msungwanayo siyikukhudza mtsutso umenewo ayi. Apapa mwanayu akungofuna khothi limasulire ngati angathe kuchotsa mimba yakeyo,” atero a Kaiyatsa.

Yemwe akuyendetsa nkhaniyo ku bungwe la CHRR a Dennis Mwafulirwa adati mkulu yemwe adagwiririra msungwanayo adagwidwa ndipo akusewenza zaka 14 koma adati pali chiletso cha khothi choti zambiri za msungwanayo zisaululidwe.

“Pali nkhani yachitetezo cha msungwanayo monga mudziwa kuti ndi mwana wamng’ono ndiye a khoti aletsa kuulula zina ndi zina. Chomwe tikuwopa kwambiri nchoti ena akamva za komwe amachokera kaya mbiri ya sukulu akhoza kumufufuza mpaka kumupeza,” atero a Mwafulirwa.

Koma iwo ati nkhaniyo itangochitika, ofesi yowona zachisamaliro cha ana idatenga msungwanayo nkukamusungitsa ku nyumba yachitetezo chifukwa cha chitonzo chomwe amalandira m’mudzimo komanso yemwe adamupanga chipongweyo amakhala mmudzi momwemo.

Chikalata chomwe mabungwewo adatulutsa limodzi chikuti mimba zobwera kaamba kogwiriridwa zimakhala n’ziopsezo zambiri pa moyo wa wogwiriridwayo.

“Munthu akagwiriridwa chiopsezo choyamba n’kusalidwa m’mudzi komanso poti ena amakhala achichepere, moyo wawo umakhala pa chiopsezo, ena monga mwamva kale amakhala ndi malingaliro odzipha,” chatero chikalatacho.

Mabungwewo ati kuunikira kwa khoti pa nkhani ya msungwanayo kukhoza kutsegula khomo la ufulu wa asungwana ambiri omwe amatenga mimba kaamba kogwiliridwa koma amakakamizidwa kusunga mimbayo poopa malamulo.

Related Articles

4 Comments

  1. Strah is the epitome of fearless metal greatness! Joining this global community of passionate metalheads has been a game-changer for me. The connections, exploration, and celebration of our shared fearlessness are beyond compare. Let’s keep this metal journey alive – who’s in? #Strah #fearnomusic

Back to top button
Translate »