Chichewa

Mfutso mpatali

Chilimwe chikuyandikira ndipo chakudya cha ziweto chili paliponse.

Mkulu wa zaulimi wa ziweto m’boma la Kasungu akuti apa ndi pamene alimi a ng’ombe akuyenera kuchita machawi kupanga mfutso kuti asadzavutike m’chirimwe pamene chakudya cha ziwetochi chimadzasowa kwambiri.

Malingana ndi mphuzitsiyo, kukonza mfutso kumathandizira kuti ziweto zizipeza chakudya chokwanira ndi chopatsa thanzi kwa chaka chonse.

“Alimi akhoza kupanga mfutso wa mtundu wa heyi kapena sayileji malingana ndi kusankha kwawo. Chifukwa choti mfutsowu umakhala wosiyana kumbali ya michere chifukwa cha kapangidwe kake, kwa omwe angakwanitse kupanga mitundu yonseyi zidzawachitira ubwino koposa,” iye adatero.

Mkuluyu adati nthawi yabwino kupanga mfutso m’madera ambiri a m’dziko muno ndi February, March ndi April.

Mwasinga adati izi zili chomwechi chifukwa udzu umakhala  ukupezeka ochuluka.

Alimi a ng’ombe ochenjera padakali pano akukonza mfutso

“Anthu ambiri m’nyengoyi makamaka amayi amakhala  kalikiliki kupanga mfutso wa ndiwo za masamba ndi cholinga choti asadzavutike nthawi ya chilimwe. Alimi a ziweto monga ng’ombe akuyenera kutengerapo phunziro ndi kumachita chimodzimodzi chifukwa nyengoyi ikafika, ziweto zimapengetsa,” iye adatero.

Mkuluyu adati kufutsa udzu m’njira ya heyi kapena sayileji kumatetezera kuti michere isachokemo kusiyana ndi kulekelera udzu kuti uzingodziumira  m’munda.

Mlimi wina wa ng’ombe za mkaka kwa Goliyati m’boma la Thyolo Taulo Chisoso adati kupanga heyi kapena sayileji ndi kopepuka kusiyana ndi kusaka udzu  m’nthawi ya chirimwe.

Iye adati m’nyengoyi, zimamutengera kanthawi kochepa chabe kuti akonze mfutsowu chifukwa udzu umapezeka paliponse.

“Chifukwa choti ndimakonza mfutso, m’chirimwe ndimakhala mfulu choncho ndimangotapa n’kumadyetsera ng’ombe zanga osadandaula nawo za kusowa kwa chakudya,” iye adatero.

Iye adati izi zimamuthandizira kupeza mkaka wochuluka kuchokera ku ng’ombe zake kwa chaka.

Mwasinga adafotokoza  kuti kusiyana kwa heyi  ndi sayileji n’koti  sayileji safuna dzuwa pamene heyi amafuna dzuwa.

“M’Chingerezi muli mawu woti make hay while the sun is shining kutanthauza kuti heyi  amafuna dzuwa lokwanira kuti asatenge nthawi yaitali kuuma ndipo lamulo lake ndil loti mlimi ayanike  kwa masiku awiri okha.

 “Izi zimathandiza kuti michere yofunikira isachokemo koma madzi okha  choncho amayenera kulongezedwa akangouma,” iye adatero.

Mwasinga adaonjeza kuti alimi amayenera kupanga heyi kapena sayileji  pamene udzu ukupota ndipo ngati  akugwritsa ntchito chimanga, adule chikangobereka kumene  chisadakhwime.

“Udzu woterewu umakhala wabwino  chifukwa zakudya zambiri zimakhala zili ku masamba pomwe  ukabereka komanso njere zake zikakhwima,  zimakhala zapita ku njerezo,” iye adatero.

Wa zakafukufuku wa ziweto ku nthambi ya zakafukufuku wa zaulimi ya Bvumbwe m’boma la Thyolo Mphatso Suman adathirirapo ndemanga kuti chifukwa choti mfutso wa heyi umakhala ouma bdi olimbirako, alimi amayenera kumathira molase ndi mchere pamene akudyetsera.

Iye adati izi zimathandiza kuti mfutsowu udyedwe mosavuta chifukwa umafewa.

“Kuonjezera apo, mamolasi ndi mchere umakometsa mfutsowu choncho ng’ombe zimadya onse osasiyako koma mlimi akangopatsira osathira izi wambiri umangotsa zotsatira zake sizikhala ndi thanzi,” iye adatero.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Back to top button