Nkhani

Mitala iphetsa

Listen to this article

Mayi wa zaka 19 wadzipha ku Kasungu atazindikira kuti mwamuna yemwe adakwatirana naye pokhulupirira kuti banja lake loyamba lidatha ndi mkazi wake akupangabe chikwati ndi mkaziyo mwa mseri.

Izi zachitika m’mudzi mwa Matatiyo, mfumu yayikulu Mangwazu m’bomalo komwe mayi Mtisunge Makwinja adakakwatiwa ndi mwamuna yemwe adamuuza kuti banja lake loyamba lidatha ndi mkazi wake.

Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Kasungu a Miracle Mkozi ati banja latsopanolo litayamba, Makwinja adazindikira kuti mwamuna wakeyo akuzemberanabe ndi mkazi wake wakale ndipo iye adachenjeza mwamunayo kuti asiye.

“Zikuoneka kuti mwamunayo sadafune kusiya kuyenda ndi mkazi wake woyambayo mpaka pa 18 November kudabuka mkangano pakati pa mwamunayo ndi Makwinja pankhaniyoo,” atero a Mkozi.

Iwo ati pa 19 November 2023, banjalo lidapita kumunda limodzi koma malemu Makwinja adanyamukako changu kusiya bamboyo akugwirabe ntchito kumundako ndipo iye atafika kunyumba adamwa mankhwala omwe sadadziwike.

A Mkozi ati anthu a chifundo adatengera a Makwinja kuchipatala cha Kasungu komwe adafikira kuuzidwa kuti mayiyo adali atamwalira kale ndipo chomupha chidali mankhwala omwe akuganiziridwa kuti adamwawo.

Malingana ndi a Mkozi, malemu a Makwinja amachokera m’mudzi mwa Katema kwa mfumu yayikulu Kaomba m’boma la Kasungu lomwelo.

Gawo 17 la malamulo a dziko lino lokhudzana ndi mabanja komanso kutha kwa mabanjawo limati polowa m’banja lodziwika ku boma munthu amayenera kuulula chilungamo ngati sali pa banja ndipo gawo 51 la malamulo omwewo limati munthu yemwe walowa m’banja ali kale pabanja lina koma sadaulule akapezeka wolakwa amayenera kulipira K100 000 kapena kukasewenza zaka 5.

Izi zili apa, phungu wa kummwera m’boma la Lilongwe a Peter Dimba a Malawi Congress Party (MCP) apempha boma kuti lichotse mlandu wa anthu ofuna kudzipha chifukwa nthawi zambiri anthu ofika apa amakhala kuti sakuganiza moyenera ndipo akufunika thandizo lina osakhala chilango.

Polankhula m’nyumbayo popereka maganizo awo pa lipoti la momwe kaganizidwe ka ngwiro kalili m’dziko muno, a Dimba adati nthawi zambiri anthu amafuna kudzipha kaamba ka zifukwa zoti kuziunikira bwino zimakhala zomveka.

“Kuti munthu afike poganiza zodzipha ndiye kuti zinthu zathina osati masewera. Zoti anthu ofuna kudzipha azimangidwa sizitithandiza,” adatero iwo.

Theka loyamba la chaka chino, anthu 256 adadzipha m’dziko muno poyerekeza ndi 135 chaka chatha.

Related Articles

Back to top button
Translate »