Nkhani

Mkulu wa zaka 22 akaseweza zaka 23

Listen to this article

Wakhala akuthyola nyumba masana kasanu konse ndi kubamo katundu. Anthu ku Balaka akhala akumusaka koma adali woterera ngati mlamba. Koma la 40 lamukwanira John Bunaya, wa zaka 22, amene bwalo la milandu lamuthowa ndi zaka 23 kuti akaseweze kundende chifukwa cha kutolatola.

Wapolisi woimira boma pamilandu, Inspector Isaac Mponela, wati bwalo la Balaka lidapeza mkuluyu wolakwa pamilandu yonse isanu yomwe adapalamula.arrest

Mponela adauza bwalolo kuti pa 3 March, chaka chino, masanasana dzuwa likuswa mtengo, Bunaya adaswa nyumba ya Gloria Mphwiyo ndi kubamo njinga ya komanso matumba awiri a chimanga. Zonse zidali za mtengo wa K43 000.

Pa 28 March, chaka chonchino, Bunaya akutinso masanasana adaswa nyumba ya Ruth Marley ku Majiga m’bomalo ndi kubamo wailesi komaso zovala ndi katundu wina.

Bunaya pa 13 April, akuti adaphwanyanso nyumba ya Rachel Jika ndi kubamo laputopu, matilesi, mafuta ophikira ndi shuga za K320 000.

Pa 10 May, Bunaya akuti adaswa nyumba ya William Munthali ndi kubamo kamera, foni ndi zakugolosale za K72 000.

Iye sadalekere pomwepo. Pa 13 May akuti njondayi idakaswanso nyumba ya Daniel Pondani komwe adakasokolotsa DVD, masipika awiri a LG, mafuta ophikira ndi mafoni za K100 000.

Mponela atamaliza kumunenera Bunaya kubwaloko, anthu adadzidzimuka. Izi zidadabwitsanso woweruza milandu, Victor Sibu, yemwe sadachedwe koma kusatakula chilango chokhwima.

Iye adalamula Bunaya, yemwe adavomera kulakwa pamilandu yonseyi, kuti akaseweze zaka 23 ngakhale iye adaliralira kuti ndi wachichepere komanso ndiye amasamala banja lake ndi makolo omwe adati ndi okalamba.

Bunaya amachokera m’mudzi mwa Kandengwe kwa T/A Nsamala m’bomalo.

Related Articles

Back to top button
Translate »