Nkhani

Mlandu wa a Bushiri ukhalako pa Julayi 10

Listen to this article

Mlandu wa a Pulofeti Shepherd Bushiri ndi akazi awo a Mary unalephereka kuyamba Lachiwiri kaamba ka kusagwirizana kumene kunalipo pakati pa maloya awo ndi a boma.

Mlanduwu unali ku Lilongwe.

Pa chifukwa chimenecho, woweruza milandu a Madalitso Chimwaza adauimitsa ndi kulamula kuti udzapitilire pa 10 Julayi 2023.

 Loya wa a Bushiri a Wapona Kita adati mlanduwo sungayambe chifukwa mbali yoimira boma idali isadapereke umboni onse ofunika.

“Mukudziwa kuti bwalo lino lidakumananso pa 16 Feburuwale 2023 pomwe khoti linagamula  kuti boma litipatse umboni omwe lili nawo koma sitidalandile,” iwo adatero.

 Koma woimira boma a Dzikondianthu Malunda adati a Kita adawadzidzimutsa chifukwa zomwe adanena mukhothizo amayenera kuwadziwitsa powalembera tsiku lakukhothi lisadafike.

“M’kuwona kwanga, zomwe abweretsa anzathuwa ndiye mutu wa mulandu wonse. Choncho amayenera kutidziwitsa m’ndondomeko yake kuti tikonzekere bwino tisanabwere ku khoti,” iwo adatero .

A Chimwaza atamva mbali zonse, adagamula kuti payenera kutsatidwa malamulo a khoti.

 Iwo adapereka masiku 14 kuti achite zofunikira komanso masiku ena 14 oti maloya a boma aunike mfundozo.

Izi zidachititsa kuti mboni yochokera m’dziko la South Africa a Sibongire Mnzinyathi asathe kuperekera umboni.

A Kita amafuna kuti khothi lingothetsa mlanduwo osamva n’komwe umboni uliwonse chifukwa adati mbali ya boma idalephera kupereka zofunikira.

M’mwezi wa Novembara 2020, a Bushiri ndi akazi awo adathawa ku South Africa n’kubwera ku Malawi ati chifukwa amaopsezedwa pomwe dzikolo linkawazenga milandu.

 Mulanduwo ukadali pa siteji yofuna kupeza ngati ungakambidwe kapena ayi. Maloya a a Bushiri adapempha khothi kuti ngati n’kukambidwa, ndiye kuti mboni zaku South Africa pa ziyenera kubwera ku Malawi.

Koma panthawiyo,woweruza milandu a Redson Kapindu adati mbonizo zikhoza kuperekera umboni kudzera pa makina a Internet kapena dziko la Malawi likhoza kupempha khothi lapadera ku South Africa kuti limve umboni.

A Bushiri, womwe adayambitsa mpingo wa Enlightened Christian Gathering (ECG) apangapo utumiki wa Mulungu m’maiko osiyanasiyana. Koma adakakhazikika ku South Africa komwe ankayendetsera bizinesi zawo.

Related Articles

Back to top button