Mnzanga akusokoneza banja langa
Ndili pa banja ndipo ndili ndi ana. Ana anga onse amapita sukulu za pa mwamba chifukwa choti bambo awo amawalipirira.
Ndili ndi mnzanga yemwenso ali pa banja ndipo timacheza kwambiri. Timatha kukambirana nkhani zachinsisi zathu. Takhala tikucheza nthawi yaitali kwambiri. Tinadziwana ku sukulu. Mose momwe timachezamu sindimadziwa kuti anzanga ali ndi mpeni ku mphasa kapena nditi anzangawa sakondwera nane.
Iwo akhala akumawauza amuna anga zosakhala bwino za ine. Zinthuzo zimakhala kuti ine sindinachite. Nthawi ina yake ndinawauza kuti ndikuchoka ndipo anandifunsa kuti amuna anu akudziwa? Ndinali wodabwa kuti bwanji akundifunsa ngati amuna anga akudziwa za ulendo wanga.
Amuna anga ndi omwe anandituma kuti ndipite kumeneko. Ataona kuti ndachoka anawaimbira amuna anga ndi kuwauza kuti ndapita ku chibwenzi pomwe amuna anga amadziwa komwe ndapita.
Anamuna anga anamuuza mnzanga uja kuti iwo ndi amene andituma koma mnzangayo anakakamira kuti sindili komwe ananditumako. Adawauza amuna anga kuti azindiyang’anitsitsa mayendedwe anga.
Mwamuna wanga adawafunsa kuti kodi makamaka mukufuna kundiuza chiyani? Ndipo iwo anati ndine mkazi wosayamika komanso wa chimasomaso. Ndiye iwo anati kuti adzandigwira okha. Izi zidamunyansa kwambiri mnzanga uja mpaka adawauza kuti iwo ndi wopepera kwambiri.
Mwamuna wanga adandifotokozera zonse ndipo adandiuza kuti tisiye kucheza. Nditasiya kucheza naye adayamba kufalitsa mbiri yoti ine ndinamudyesa mankhwala mwamuna wanga.
Nditani pamenepa azakhali?
Ine wodandaula,
Mangochi
Zikomo,
Mayi, apatu palibe chomwe mungachite kupatula zomwe anakuuzani amuna anu. Siyani kucheza nawo anzanuwo. Ndi amayi woipa.
Ndikuganiza kuti kucheza kwanu kunali kwa chilungamo koma ngati mumapanga zina ndi mnzanuyo dziwani kuti zonse ziululika.
N’kutheka kutinso inu mumamuuza zonse za m’nyumba mwanu ndi chifukwa chake adayamba kukupangirani kaduka.
Pocheza muzikhala ndi malire pa zoyankhula zanu. Osamangobwebwetuka zili zonse za m’nyumba mwanu kaya za ndalama, za ntchito ya amuna anu kapenanso za zinthu zomwe muli nazo ndi zitukuko zomwe mukufuna kuchita.
Izi zimabweretsa kaduka pakati pa anthu. Kuyambira pano, phunzirani kutseka pakamwa panu. Sindikuti musamacheze ayi, koma kumakhala osamala pocheza kuti mupewe zinthu ngati zimenezi.
Muthokoze kuti amuna anu amakukondani.
Anatchereza
Abale a makolo akutilanga
Anatchereza,
Makolo athu mmene ankamwalira adasiya pa malo pathu atabzala zipatso zochuluka kwambiri ndi mitengo ina. Abale awo a makolo athuwa ataona kuti atisiya adayamba kulowelera mitengo yathuyi. Abwela kuzadula komanso kutenga athu oti adzagule zipatsozo.
Tikamaletsa, amalankhula mawu osakhala bwino. Titatopa nazo tidapita kokasuma kwa a mfumu. Abalewa zidawanyansa mpaka kunena kuti mitengo sitinabzale ndife.
Amfumu anawauza kuti akulakwa kwambiri ndipo asiye zimene akuchitazo koma iwo sakusiyabe kudula mitengoyo ndipo ndi anthu oderera kwambiri.
Wodandaula,
Dowa.
Abale opanda chikondi nthawi zonse amatero. Ndikuganiza kuti mmene makolo anu amabzala mitengo imeneyo aliyense anali akuona. Ndipo pobzalapo iwo amadziwa kuti ali ndi ana omwe azizagwiritsa ntchito iwo akapita.
Amachita zimenezi kuti ana awo asadzavutike. Zonse akuchitazo ndi mtopola okhaokha. Pamalo paliponse aliyense amakhala ndi zinthu zake ndipo pamakhalanso malire. Iwo ngati ali alesi asapezerepo mwayi pa zithu zoti si zawo.
Ngati amfumu alephera kasumeni kwa T/A. Ngati sizitheka asiye achite zomwe akufunanso. Auzeni kuti ayizule mitengo yonse ndipo ayitenge.
N’kutheka kuti chilipo chomwe akufuna kwa inu ana. Muzipemphera kwambiri kuti Mulungu akutetezeni.
Anatchereza.