Nkhani

Moto buu! Ku Swaziland

Listen to this article

Kochi wa timu ya dziko lino ya Malawi Flames, Ernest Mtawali, wati timu yake yakonzeka kuonetsa zakuda timu ya Swaziland yomwe aphane nayo mumpikisano wa Africa Cup of Nations (Afcon) mawa lino pa Somhlolo Stadium mumzinda wa Lobamba.

Malawi ili m’gulu L momwe muli Swaziland, Guinea ndi Zimbabwe. Awa ndi masewero achiwiri a Flames mumpikisanowu chigonjerreni 2-1 ndi ndi Zimbabwe pa Kamuzu Stadium pa 13 June chaka chino. Panthawiyo kochi adali Young Chimodzi, yemwe adachotsedwa ntchito kaamba ka kugonjaku.Flames_chad

Koma Mtawali akuti anyamata ake ali bwino ndipo akuyembekezera kuphophola Swaziland, timu yomwe m’masewero ake oyamba idakatikita Guinea kwawo komwe.

“Ndili ndi chikhulupiriro mwa anyamata amene ndawatenga. Tikufuna kumwetsa zigoli chifukwa njira yabwino yoteteza golo lanu ndi kumenyera mpira kutsogolo kuti tikapeze zigoli,” adatero mmene ankanyamuka m’dziko muno Lamulungu lapitali kupita ku South Africa komwe idalepherana ndi Mbombela United 2-2 pamasewero apaubale pokonzekera Swaziland.

Malawi yakumanapo ndi Swaziland maulendo 18 ndipo yapambana katatu, kugonja ka 10 ndi kulepherana mphamvu kasanu.

Mumpikisanowu chaka chatha Malawi sidachite bwino pamene idakumana ndi matimu akuluakulu m’gulu lawo monga Algeria, Mali ndi Ethiopia. Pamasewero onsewo, Malawi idangokwanitsa kupeza mapointi 7 itapha Mali pakhomo komanso Ethiopia ndi kulepherana ndi Ethiopia kwawo.

Koma Mtawali akuti timu yomwe ali nayo pano ndi ina ndipo chiyembekezo chilipo kuti mawa alandira zotsatira zabwino kuchokera kwa anyamata ake.

Mtawali watenga Limbikani Mzava, Stanly Sanudi, Yamikani Fodya, Wonder Jeremani, John Lanjesi, Pilirani Zonda, Yamikani Chester, Isaac Kaliati, Chimango Kaira, Chawanangwa Kaonga, Chiukepo Msowoya, Muhammad Sulumba, Manase Chiyesa, Robin Ngalande, Robert Ng’ambi, John CJ Banda, Chikoti Chirwa, Micium Mhone, Gerald Phiri jnr Richard Chipuwa Bright Munthali.

Amkhalakale monga Joseph Kamwendo, Fischer Kondowe, Esau Kanyenda, Frank Banda, Lucky Malata, Harry Nyirenda, Zicco Mkanda, Atusaye Nyondo, MacDonald Harawa ndi Charles Swini atsala.

Masewero a Zimbabwe, Malawi idachinya kudzera mwa John Banda amene mawali akhalenso ndi ntchito yaikulu pakati pa Flames.

Related Articles

Back to top button
Translate »