Nkhani

Mtima pansi—APM

Listen to this article

Ngati aMalawi adali ndi chiyembekezo choti aona kusintha kwakukulu pachuma ndi zina ndi zina zokhudza moyo wawo pambuyo pa kulumbiritsidwa kwa boma latsopano lotsogozedwa ndi Pulezidenti Peter Arthur Mutharika ndi chipani chake cha DPP, asathamange magazi chifukwa izi sizitheka lero ndi lero.

Izi zili choncho chifukwa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika Lachiwiri adati aphungu a Nyumba ya Malamulo sakambirana ndondomeko ya chuma cha dziko lino (Bajeti) yomwe imayenera kuyamba pa 1 July, 2014 mpakana pa 31 June 2015.

Peter_dppPolankhula koyamba ngati mtsogoleri wa dziko lino m’Nyumbayo, Mutharika adati mmalo mwake ndondomekoyi adzaikambirana mwezi wa August pofuna kupereka mpata woti boma liunike bwinobwino kunthambi zosiyanasiyana zinthu zofunika mundondomekoyi.

Iye adati mmalo mwake aphungu angokambirana za ndondomeko ya chuma chapadera chomwe boma ligwiritse ntchito kuyambira mwezi wa July mpakana September, 2014.

“Gawo 178 la malamulo oyendetsera dziko lino limalola kukhala ndi ndondomeko yongoyembekezerayi. Tinali ndi nthawi yochepa yokonza ndondomeko ya chaka chonse. Komanso tiyenera kuunikira bwino ndalama zomwe zatsala kuthunba la boma tisanakonze ndondomekoyi,” adatero Mutharika.

Nduna ya zachuma Goodall Gondwe akuyembekezeka kukapereka ndondomeko yoyembekezerayi sabata ya mawa.
“Tikapereka ndondomekoyi tikhala tikufunsa anthu zimene akufuna kuti tiganizire mundondomeko ya chuma ya chaka chonse,” adatero Gondwe.

Mwa zina, Amalawi ambiri chidwo chawo chagona poti boma la Mutharika litsitsa liti mitengo ya malata ndi simenti kuti osauka amene akugona nyumba zofoleredwa ndi udzu komanso zozira ndi donthi nawo athe kumanga zofolera ndi malata komanso zasimenti pansi.

Pokopa anthu kuti adzachivotere chipanichi panthawi ya kampeni zisankho zisadachitike pa May 20, 2014, akuluakulu adalonjedza Amalawi kuti chipani cha DPP chikadzakhalanso m’boma chimodzi mwa zinthu zoyambirira pofuna kutukula miyoyo ya Amalawi ku kutsitsa mitengo ya malata ndi simenti kuti aliyense azigona m’nyumba yoyenerera.

Akatswiri m’nthambi zosiyanasiyana m’dziko muno ati boma lingachite bwino pachitukuko cha dziko litatsata bwino mfundo zomwe Mutharika adanena potsegulira Nyumbayo.

Akatswiriwa ati Mutharika adanena mfundo zabwino zokhudza chitukuko koma sadatambasule bwino momwe mfundozo bioma lidzakwaniritsire.
Zina mwa mfundo zomwe akatswiriwa ayamikira ndi zotukula ntchito za umoyo, ulimi ndi maphunziro koma ati sizikutambasula bwino mmene zidzayendere.

Dalitso Kubalasa, mmodzi mwa akatsiwiriwa, yemwe ndi mkulu wa bungwe la Malawi Economic Justice Network lomwe ntchito yake ndi kuona mmene boma likuyendetsera chuma kuti chipindulire aliyense, wati boma lakhazikitsa mfundo zabwino kwambiri koma lalephera kufotokozera Amalawi mmene zidzayendetsedwere.

“Mfundozi ndizabwino kwambiri pachitukuko cha dziko lino ndipo n’zosangalatsa kuti mtsogoleri akudziwa za mavuto omwe alipo pachuma. Koma ngakhale zili choncho, pali mfundo zina zofunika kuwongoledwa bwino kuti zigwire bwino ntchito yake,” adatero Kubalasa pocheza ndi Tamvani Lachiwiri lapitali.

Pankhani za umoyo, Mutharika adati, mwa zina, boma lidzakhazikitsa chisamaliro chapadera cha anthu ogwira ntchito m’boma komanso lidzatukula miyoyo ya anthu ogwira ntchito m’boma pakakwenzedwe pantchto ndi malipiro.

Mkulu wa bungwe loona kuti ntchito za umoyo zikufikira anthu onse mofanana la Malawi Health Equity Network (Mhen), Martha Kwataine, akuti boma laganiza bwino pokhazikitsa chisamaliro chapadera cha anthu ogwira ntchito m’boma, koma wadzudzula kuti silidatambasule bwino makamaka pa nthawi yomwe ntchitoyi idzayambe.

“Izi ndi zomwe takhala tikumenyerera kwa nthawi yaitali ndipo apa boma laganiza bwino kwambiri makamaka pakulonjeza kutukula miyoyo ya anthu ogwira ntchito za chipatala.

“Koma chomwe ndingapemphe boma ndi kutambasula bwinobwino nthawi yomwe izi zidzayambe kusiyana ndi kuti anthu azingokhala mumdima,” adatero Kwataine.

Mutharika adatinso boma lidzalimbikitsa ntchito zotukula achinyamata pokhazikitsa malo ophunzitsa achinyamata ntchito zosiyanasiyana kuti azikhala odzidalira paokha.

Nduna yakale ya zachuma, Mathews Chikaonda, adati boma likuyeneranso kubwera poyera mmene ntchito yotukula achinyamatayi idzakhalire.

Iye adati achinyamata ndi ofunika kwambiri pachitukuko cha m’dziko choncho n’kofunika kuika patsogolo ntchito zowatukula.

Related Articles

Back to top button
Translate »