Nkhani

Mutharika asankha nduna

Listen to this article

Pangotha maola sipikala wa Nyumba ya Malamulo Richard Msowoya atagwirizana ndi atsogoleri a zipani za m’Nyumba ya Malamulo kuti asankhe komiti yoti iziyendetsa zochitika m’Nyumbamo kaamba ka kusowa kwa nduna, mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adasankha nduna zina mbandakucha wa Lachinayi.

Zinthu zidaima m’Nyumbayo Lachitatu pomwe aphungu adasowa chochita chifukwa komiti yomwe imasankha nkhani zimene aphungu akambirane patsiku padalibe. Komitiyo imayenera kukhala ndi wapampando yemwe ndi nduna ya boma.

Msowoya adaimitsa msonkhano wa aphunguwo kuti ayambenso kukambirana 9:30 Lachinayi koma pomwe kumacha n’kuti Mutharika atasankha nduna zatsopano 9 zimene zidalumbiritsidwa cha m’ma 8.

Mwa ndunazi, amayi ndi awiri: Dr Jean Kalirani, amene ndi nduna ya zaumoyo komanso nduna ya zamasewero, achinyamata ndi chikhalidwe Grace Obama Chiumia. Chiumia ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa aphungu a kumbali ya boma.

Ndipo nduna 6 n’zochokera m’chigawo cha Kumwera, ziwiri za Pakati pomwe ziwiri, tikaphatikizapo nduna ya zachuma Goodall Gondwe yemwe adali woyambirira kusankhidwa nduna, ndi za Kumpoto.

Samuel Tembenu, yemwe ndi nduna ya zalamulo ndi nduna yokhayo imene si phungu. Iye adalephera kupeza mpando wauphungu ndi mavoti ochepa kwambiri m’dera la pakati ku Salima. Izi zikusonyeza kuti Mutharika wasankha nduna ziwiri zomwe si aphungu chifukwa nduna ya zachuma Goodall Gondwe amene adasankhidwa pampandowo mmbuyomu adalephera kupeza mpando wa uphungu kumpoto m’boma la Mzimba.

Nduna ya zamtengatenga ndi Francis Kasaila, amene adalephera kukhala sipikala wa Nyumba ya Malamulo atagonja kwa Msowoya Lolemba, pomwe nduna ya zofalitsa nkhani ndi Kondwani Nakhumwa. Nduna ya zaulimi ndi Dr Allan Chiyembekeza, yemwe adali wapampando wa komiti ya zaulimi m’Nyumba ya Malamulo ya pakati pa 2009 ndi 2014.

Henry Mussa, amene ndi mkulu wa aphungu a boma m’Nyumbayo ndi nduna ya zantchito, pomwe Emmanuel Fabiano, amene adakhalapo mkulu wa sukulu ya ukachenjede ya Polytechnic, ndi nduna ya maphunziro. George Chaponda ndi nduna yoona za maiko akunja.

Izi zikusonyeza kuti boma la Mutharika tsopano likuyendetsedwa ndi anthu 12, kuphatikiza mtsogoleri wa dziko linoyu ndi wachiwiri wake Saulos Chilima. Mwandunazi, zisanu zidakhalapo nduna m’boma la mkulu wake wa mtsogoleri wa dziko Bingu.

Mkulu wa bungwe loona kuti maphunziro ndi apamwamba la Civil Society Education Coalition Benedicto Kondowe adati kusankha nduna zambiri zochokera dera limodzi kungachititse kuti madera ena asapindule.

“Ndunazi zikhoza kumakondera madera awo pachitukuko, choncho madera ena angamve kuwawa ndi ulamulirowu,” adatero Kondowe.

Ndipo mmodzi mwa akadaulo pa ndale Mustafa Hussein adati ambiri mwa omwe adasankhidwawo, ena adali mu ulamuliro Bingu.
“Nkhope zina tidazionapo koma zidalephereratu mu ulamuliro wa Bingu. Tikudabwa kuti azisankhiranji. Komanso ena mwa amene abwera kumene ali ndi maphunziro okwanira ku maunduna omwe awapatsa, koma tiona momwe agwirire ntchito,” adatero Hussein. n

Related Articles

Back to top button
Translate »