Nkhani

Mtsutso pa zotsegulira sukulu lolemba

Listen to this article

Pulani ya boma yoti sukulu zikuyenera kutsegulidwanso Lolemba likudzali yasinthidwanso ndipo tsopano Unduna wa zamaphunziro ukufuna kuti uwunikenso m’mene mliri wa covid-19 ukhalire msabata ziwiri zikubwerazi.

Akadaulo ena pa zamaphunziro komanso zaumoyo akhala akupereka maganizo osiyanasiyana okhudza nkhaniyi.

Kadaulo pa zamaphunziro Limbani Nsapato wati sikoyenera kutsegulanso sukulu chifukwa mphepo ikuonetsa kuti matendawa afika paliwombo tsopano kotero chitetezo m’sukulu nchokayikitsa.

“Mwezi wa January wokha anthu opezeka ndi Covid adakwana 17 380 mwa anthu 23 963 omwe adapezeka chiyambireni mliliwu mu March 2020. Chiyambireni, anthu 702 ndiwo adamwalira ndipo mwa amenewa, 513 adamwalira mu January 2021 mokha ndiye n’kumati zili bwino?” Adatero Nsapato.

Iye adati ngakhale palibe malipoti okhuthala okhudza momwe matendawa alili m’sukulu, zotsatira za m’sukulu zina zomwe ana adayesedwa monga ku Lilongwe Girls komwe ana oposa theka adapezeka nayo n’zokwanira kutsimikiza kuti ino si nthawi yotsegulira sukulu.

Iye adaonjezera kuti maso asakhale pa ana okha komanso aphunzitsi omwe ambiri ndi achikulire ndipo ali m’gulu la anthu omwe ali pachiopsezo chachikulu ku matendawa.

“Ana ambiri akhoza kukhala nayo koma osaonetsa zizindikiro n’kumangofalitsa komanso anawo akapezeka, owasamala ndi aphunzitsiwo ndiye aphunzitsi atatenga, mwayi wopulumuka ndi wochepa potengera msinkhu wawo,” adatero Nsapato.

Nsapato adagwirizana ndi kadaulo mnzake Steve Sharah yemwe adati sukulu zisadatsegulidwe pakuyenera pakhale mlingo wa njira ya sayansi wolinga kafalidwe ka Covid ndi kuthekera kopulumutsa ana ndi aphunzitsi.

“Komiti ya Pulezidenti pa za Covid ikuyendetsa kale nkhani yopanga mlingo ndipo pokhapokha mlingowo utadziwika ndi kuwugwiritsa ntchito, sitinganene pano kuti titsegulire sukulu kapena ayi,” adatero Sharah.

Koma kadaulo pa zaumoyo George Jobe adati chokhacho choti boma lakhala likusunga ana ena kusukulu makamaka zogonera komweko chikutanthauza kuti n’zotheka kutsegulira sukulu chifukwa ndiye kuti chitetezo chiliko.

Iye wati umboni wina ndi woti boma lidakwanitsa kulembetsa mayeso a Fomu 4 mpaka kumapeto ndiye chovuta palibe kutsegulira sukulu koma pakhale mgwirizano wa magulu onse okhudzidwa kuti chitetezocho chikule.

“N’zongofunika makolo, aphunzitsi, a makomiti a sukulu, mafumu ndi unduna wa zamaphunziro agwirane manja basi. Apa tikunena za ana oti ena angoyendayenda m’makukamu tsono n’kwabwino ali kusukulu chifukwa kumeneko amamangika,” adatero Jobe.

Boma likuyenera kuyamba kupereka katemera wa Covid mwezi wa mawa wa March koma Jobe wati kutsegulira sukulu sikungadikile katemera chifukwa ngakhale abwere, si onse omwe adzalandire koyambilira.

Pulezidenti wa bungwe la sukulu zomwe si zaboma Joseph Patel wati zikhala zodandaulitsa ngati boma silitsegura sukulu Lolemba momwe Pulezedenti Lazarus Chakwera adalengezera.

“Tikuloweraku, ana ambiri asiyira sukulu panjira chifukwa cha mimba, mabanja komanso ena ataya chidwi ndi sukulu. Tidakwanitsa kutsegulira mu August 2020 Covid ali mkati ndipo zidatheka tsono chingativute pano nchiyani?” Adatero Patel.

Iye adati nkhani yabwino ndi yoti ana ambiri omwe adapezeka ndi zizindikiro za Covid tsopano ali bwino komanso eni sukulu adakonzekera mokwanira kukhwimitsa chitetezo m’sukulu.

Koma makolo ena ati boma lingopanga ganizo limodzi n’kuligwiritsitsa kusiyana n’kumasiya anthu m’malere chifukwa zikusokoneza zambiri.

“Tikadangodziwa mutu weniweni ngati kuli kutsegulira atsegule kapena atiuze zomveka. Nafe makolo tikukhudzidwa chifukwa kuti anawo apite kusukulu ndife ndiye timayenera kupanga mabajeti athu bwino. Izi zomati mwina sizitithandiza,” adatero Wilson Jemitale wa ku Lilongwe.

Related Articles

Back to top button