Nkhani

Mvula iwononga katundu ku Phalombe

Listen to this article

Inde mvula ndi madalitso, komabe kwa anthu a ku Phalombe ndi Mulanje madalitsowa akuwalandirira kulimba.

Ngozi zogwa mwadzidzidzi zafika pena kumeneku. Mu November kudali ku Mulanje komwe anthu 500 adakhudzidwa. Pano ndi ku Phalombe komwe anthu 279 akusowa pogwira mvula ya mphepo itasasula nyumba zawo.

Wothandizira kwa wamkulu woona ngozi zogwa mwa dzidzidzi ku Phalombe Dave Chibani akuti mavutowa adayamba pa 18 December ndipo kufika pano anthuwo sadalandirebe thandizo.

“Tawalembera kale anthu oyenerera kuti atithandize. Zinthu sizili bwino, kufika lero [31 December] sitidalandire thandizo lililonse,” adatero Chibani.

Nako ku Mulanje anthu adakasowa pogwira. Nyumba zidasasuka ndipo anthu ena kuvulazidwa pothawira malo oti azembe ngoziyo.

Padakalipano, Chibani wati podikira thandizo, alimbikitsa kupereka mitengo kwa makomiti amene amaona ngozi zigwa mwadzidzidzi.

Mitengo 800 ndiyo yagawidwa kwa makomitiwa m’boma la Phalombe mwa ma T/A 6. “Mitengo imathandiza ngozi monga izi, komanso mitengoyi iwapatsa ubwino wina akabzala chifukwa ndi ya zipatso.

“Sitinangowapatsa koma tinawaphunzitsa, bungwe la Concern Universal ndi bungwe la Irish Aid ndilo lidatipatsa mitengoyi kotero zitithandiza ndi ngozi yachitikayi chifukwa anthu amene tawapatsawo ndiwo amatithandiza kukachitika ngozi za dzidzidzi,” adatero Chibani.

Related Articles

Back to top button