Nam yapindulanji pa Tigresses?
Bungwe la Malawi National Council of Sports tsopano layeretsa timu ya Tigresses kuti Nam ndiyo yolakwa pankhani yoti timuyi ichotsedwe m’chikho cha Presidential Initiative for Sports chifukwa idaseweretsa wotupa mchombo.
Tithokoze kuti chilungamo chadziwika ndipo timuyi ipikisanabe m’chikho cha apulezidenti.
Tilangizeko Nam kuti sibwino kuchita zinthu mwa nkhwidzi, zigamulo zinazi tiyeni tizilowa mmalamulo chifukwa zikusokoneza.
Taonani chikho cha apulezidenti chidayima pamene timati tikupseda. Onaninso kuti osewera a timuyi asiyidwa ku Australia. Ndalama zawonongeka komanso mwasokoneza timu ya dziko lino.
Nam sibwino kumaonetsa poyera matimu amene mumakwera. Kukhala ndi timu yapamtima sikoletsedwa koma zimafunika kuti matimu onse azithandizidwa mofanana.
Zotere musadzachitenso, aka kakhale komaliza. Pajatu timuyi ili panambala yoyamba mu Africa muno ndiye sitikufuna ichoke pamenepo. Mwaphunzirapo kanthu chonde sinthani kusanade.
Tifunire zabwino zonse timu ya dziko lino yomwe ili m’dziko la Australia kukapikisana ndi matimu ena anayi. Mary Waya ndi Griffin Saenda gwirani ntchito ndi osewera 12 mwatengawo ndipo ife tikuyembekezera zabwino.
Aganyu m’sabatayi timakambirana za mphunzitsi wabwino m’dziko muno. Zikuonetsa kuti aphunzitsi odziwa ntchito alipo amene mwina utawapatsa mwayi atha kunyamula Flames.
Aganyu ambiri akukambabe za mphunzitsi wakale Kinnah Phiri kuti ndiye wabwino. Ena akukamba za Elijah Kananji wa Blantyre United. Pamene Fam ikusakasaka mphunzitsi wa Flames, chonde tawunguzani m’dziko muno.