Nkhani

Ndale zimasokoneza ntchito zathu—MPS

Malawi Police Service (MPS) yavomera kuti mmbuyomu imalephera kugwira ntchito zawo mwaukadaulo kaamba ka andale omwe amalowerera kwambiri pa ntchito zawo.

Mkulu wa polisi George Kainja sabata yatha adauza Amalawi kuti afukula milandu yonse ya mgonamgona zomwe zinadabwitsa anthu ndipo ena akhala akufunsa kuti kodi n’chifukwa chiyani apolisi samachitapo kanthu pa milanduyo.

Poyankha nkhaniyi, mneneri wapolisi m’dziko muno James Kadadzera adati mmbuyomu ntchito zawo sizimayenda bwino kaamba koti atsogoleri ena andale amalowerera mpaka kusokoneza kafukufuku wawo.

“Nkhani zina zimagonera kaamba koti kafukufuku adali mkati, koma zina zimasokonekera kaamba koti andale alowererapo,” adatero Kadadzera.

Ina mwa milandu yogonera ndi imfa ya wophunzira wa ku Polytechnic Robert Chasowa, kuphedwa kwa wogwira ntchito ku bungwe la Anti-Corruption Bureau (ACB) Issa Njauja.

Anthu ambiri akhalanso akudandaula ndi kugwiririridwa kwa atsikana ndi amayi kwa Msundwe ku Lilongwe, komanso kuphedwa kwa Lule Buleya m’manja mwa apolisi mu February 2019.

Buleya, yemwe amamuganizira kuti akudziwapo kanthu pa kuphedwa kwa mnyamata wa chialubino wa m’boma la Dedza, adaphedwa atangoyamba kupereka umboni wake m’khoti.

Mboni 6 zidapereka kale maumboni awo ndipo akuluakulu ena a boma lakale adatchulidwamo pambuyo pake mlanduwu udazilala.

Koma posachedwa Tonse Alliance itatenga boma, mlanduwu udaudzutsanso ndipo apolisi 13 omwe akuwaganizira kuti akukhudzidwa ndi imfa ya Buleya adawamanga kuphatikizirapo mkulu wa polisi m’chigawo chapakati Evelista Chisale.

Lachitatu lapitali apolisi adamanga yemwe adali mkulu woteteza mtsogoleri wakale wa dziko lino, Norman Chisale, pomuganizira kuti akukhudzidwa ndi imfa ya Njauju.

Kafukufuku wa Njauju adangoima kufikira pa June 27 2020 pamene boma lidasintha manja kuchokera ku Democratic Progressive Party (DPP) kupita ku la Tonse Alliance.

Polumbira mtsogoleri wa Tonse Alliance, Lazarus Chakwera, adatsindika kuti boma lake lithana ndi ziphuphu ndi katangale.

Sabata yatha Chakwera adatsindikanso kuti boma lake silimvera chisoni aliyense amene adakwangwanula ndalama za boma.

Kadaulo pandale Ernest Thindwa adati atsogoleri ambiri amaoneka ngati abwera ndi moto pa nkhani yothana ndi katangale, koma pakupita pa nthawi palibe chogwirika chomwe amachitapo.

“Sindikuti zikhala choncho, chifukwa zonse zimatengera chikumbumtima cha mtsogoleri ndiye tiyeni tionere limodzi nzeru zomwe a Chakwera abwera nazo,” adatero Thindwa.

Iye adati mchitidwe wa ziphuphu ndi katangale utha kuchepa m’dziko muno Nyumba ya Malamulo itapanga malamulo othandiza kuti nthambi za polisi ndi ACB zikhale zoima pazokha.

Naye mkulu wa bungwe la Centre for Democracy and Economic Development Initiative (CDEDI) Silvester Namiwa  adati n’zotheka kupitiriza momwe layambiramu.

“Nkhani yaikulu ndi yoti mtsogoleri wa dziko lino a Chakwera akhwefule zina mwa mphamvu zawo kumbali yosankha mkulu wa apolisi, asirikali ankhondo ndi mkulu wa bungwe la ACB, komanso pakhale lamulo loteteza nthambizi,” adatero Namiwa.

Iye adapempha kuti pakhale ndondomeko zomveka bwino zosankhira akuluakulu m’maudindo kuti azigwira ntchito momasuka.

Sabata yatha Chakwera adati awonetsetsa kuti papangidwa malamulo othandiza kupititsa patsogolo ntchito ya apolisi, komanso ogwira ntchito ku ACB.

“Tiika chidwi chathu popanga malamulo opititsa patsogolo ntchito za nthambi za polisi ndi ACB ndi cholinga choti azigwira momasuka mosayang’anira udindo ndi nkhope ya munthu,” adatero Chakwera.

Thindwa adati ngati Chakwera akunenadi zoona ndiye kuti dziko lino ligonjetsa ziphuphu ndi katangale.

Iye adayamikira Tonse Alliance kuti nkhondo yolimbana ndi katangale yayamba bwino.

Mneneri wa DPP, Nicholas Dausi, adati Tonse Alliance ikumanga otsatira chipani chake osati chifukwa choti adalakwa kanthu, koma chifukwa chosiyana zipani za ndale.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button