Nkhani

Ndale zosadula chitukuko zikhumudwitsa aMalawi

Listen to this article
Ntchito za ulimi wamthirira za Greenbelt zidaima
Ntchito za ulimi wamthirira za Greenbelt zidaima

Kudula ntchito zimene adayambitsa atsogoleri akale a dziko lino kukuchititsa kuti Amalawi azingosaukirabe chifukwa ndalama zambiri zimangolowa m’madzi ntchitozo osamalizidwa.

Mkulu wa bungwe loonetsetsa kuti chilungamo chikutsatidwa la Justice Link Justine Dzonzi adanena izi Lachinayi mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda komanso yemwe adzaimire chipani cha MCP atanena kuti n’kofunika kuti mtsogoleri wina amene watenga mpando asamadukize ntchito za chitukuko zimene adayambitsa mtsogoleri amene wachoka pampandowo ngati zili zopindulira Amalawi.

Mapulojekiti a boma kapena othandizidwa ndi maiko ndi mabungwe ena amadilizika zipani zolamula zikasintha. Mwachitsanzo, loto la boma la UDF loti umphawi udzakhale utatheratu pofika m’chaka cha 2020 lidataidwa chipanicho chitachoka m’boma ndiponso ntchito zoti mudzi uliwonse uzitulutsa katundu wakewake ya One Village One Product (Ovop) zidalowanso pansi UDF itachoka m’boma.

Ndipo chipani cha DPP, motsogozedwa ndi Bingu wa Mutharika adakhazikitsa ntchito ya ulimi wa mthirira ya Greenbelt Initiative koma boma la Joyce Banda ndi chipani chake cha PP sakukambapo kanthu pa nkhani yolimbikitsa ulimi wakathithi m’madera oyandikira mitsinje ndi nyanja za dziko lino.

Mmalo mwake, Banda wabwera ndi ntchito zakezake monga yotukula madera a kumidzi ya Mudzi Transformation komanso yogawa ng’ombe kwa osauka ya One Family One Cow.

Izi zili choncho, ntchito ya boma ndi thandizo la ndalama zochokera ku World Bank kuti amphawi apeze malo ya Kudzigulira Malo, yalowa pansi pamene bankiyo idamaliza kupereka thandizo m’chaka cha 2011 ndipo ena mwa omwe adagula malo pa pulojekitiwo akubwerera kwawo. Nayo pulojekiti ya ulimi wamthririra ya Smallholder Irrigation Project (Ship) idafa banki yachitukuko ya African Development Bank (ADB) itapereka masikimu a mthirira atapereka sikimu za ulimiwu kwa anthu eni ake.

Dzonzi wati vuto ndi atsogoleri athu chifukwa alibe masomphenya kuti pofika zaka zikudzazi Malawi adzaoneke mwa mtundu wina.

Iye wati pa zaka 20 zapitazi dzikoli likadakhala ndi masomphenya, likadakhala pena pake koma zonsezi zikukanika chifukwa chosowa masomphenya.

“Aliyense akubweretsa zomwe akufuna zomwenso sizikupitirira, tidakabwera ndi ganizo limodzi kuti pofika chaka chakuti tikhale titakwanitsa ndi kufikira pamene takonza, pakutha pa zaka 20 bwezi dziko lino litatukuka. Nchifukwa chake tikungosaukirabe ngakhale tatha zaka 50 tili odzilamulira,” adatero Dzonzi.

Koma Dzonzi adati n’zovuta kunena kuti dziko lino laononga ndalama zingati ndi kudukiza kwa ntchito za chitukukozi.

Mmodzi mwa akadaulo pa za chitukuko, Jephter Mwanza yemwe ndi mkulu wa Kalondolondo Programme, adati kusowa umwini ndiko kumalowetsa pansi ntchitozi.

“Anthu amaona ngati ntchitozi ndi za boma, osati za iwo eni. Mwachitsanzo, anthu akhoza kumanga nyumba yopemphereramo okha ndikumaisamalira koma anthu omwewo amakanika kusamala mijigo kapena milatho yomangidwa ndi boma kapena mabungwe,” adatero Mwanza.

Iye adati kuyambitsa mapulogalamu ndi kuwaimika pa zifukwa za ndale kumaonongetsa ndalama za boma chifukwa ndalama zambiri zimakhala zitalowapo kale.

“Pulogalamu ikangoyamba, ndiye kuti ndalama zimakhala zikupita. Choncho kungoimitsa pulogalamuyo n’kunyika,” adatero iye.

Mkulu wa Ovop Tamia Kaluma-Sulumba adati pofuna kuonetsetsa kuti ntchito za bungweli sizikufa ndi kusintha kwa utsogoleri, amene ali mtsogoleri wa dziko lino amakhala wapampando wa bungweli.

“Zoonadi ntchito zina zimafa mtsogoleri akasintha. Tayesetsa kuti ntchito zathu zisafe ndi kusintha kwa utsogoleri moti tikunena pano tili ndi magulu 105. Amene angakhale mtsogoleri wa dziko lino amakhala wapampando wa bungweli, n’chifukwa chake taona atsogoleri atatu kuchokera mu 2003,” adatero Kaluma-Sulumba.

Malinga ndi Banda, si bwino kudukiza mapulogalamu chifukwa cha kusintha kwa chipani cholamula.

“N’chifukwa chake ndayesetsa kuti ndisataye ntchito zimene adayambitsa [Bingu wa] Mutharika chifukwa zina mwa izo zili ndi gawo lalikulu lotukulira dziko lino,” Banda adauza abusa amene adakamuyendera.

Ndipo polankhula pamsonkhano ku Kasungu, Chakwera ntchito za chitukuko ziyenera kuchokera kwa Amalawi eni ake.

“N’zachisoni kuti dziko lino ndi losaukitsitsa m’dera lino la Africa. Izi zili choncho makamaka chifukwa chodukiza ntchito za chitukuko. Tiyenera kukhala ndi masomphenya kuti podzafika 2020 dziko lathu lidzakhala lili pati,” adatero Chakwera.

Related Articles

Back to top button
Translate »