Opanda masiki asayende dala
Kuli cheucheu poyenda paliponse m’dziko muno kuona ngati apolisi ali pafupi makamaka kwa omwe sadachivomereze kuti masiki ikhoza kuwateteza ku matenda a Covid-19.
Kuyambira Lolemba, apolisi akhala ali kalikiliki mmalo osiyanasiyana kuphatikizapo m’misika ya m’makwalala kugwira onse wopanda masiki n’kumawalipiritsa K10 000 ngati chindapusa.
Ntchitoyi yomwe akuitcha Opaleshoni vala masiki idayamba komiti yotsogolera kulimbana ndi matendawa itatulutsa malamulo atsopano othanirana ndi Covid-19.
Malamulowo adakhazikitsidwa komitiyo itaona kuti anthu opezeka ndi matendawa akuchuluka tsiku lililonse pomwe anthu amakhwefula za kapewedwe ka matendawo.
Malingana ndi mneneri wapolisi a James Kadadzera, apolisiwo sadapange malamulo koma adapatsidwa malamulowo kuti azilimbikitsa.
“Mumadziwa ntchito yapolisi n’kuonetsetsa kuti malamulo a dziko akutsatidwa koma amapanga malamulowo ndi anthu ena. Tidalengeza kuti kuyambira Lolemba lapitali tisintha magiya ndiye anthu asatidandaule,” adatero a Kadadzera.
Koma omenyera ufulu wa anthu a Michael Kaiyatsa wa CHRR wati opeleshoniyo ndi yofunika koma apolisi adziwe mlingo wa mphamvu zawo pogwira ntchitoyo.
“N’zofunikira kuti boma lionetsetse kuti anthu akupewa Covid-19 chifukwa
Nkhani yagona poti apolisiwo ayigwira bwanji ntchitoyo chifukwa sitikufuna aziphwanyaso ufulu wa anthu,” adatero a Kaiyatsa.si nthenda yabwino.
Iwo amayankha nkhawa za anthu pa nkhanza zomwe apolisi ankachita pa opeleshoni ngati yomweyi nyengo ya mphepo yachiwiri ya matenda a Covid-19 kumayambiriro kwa chakachi.
Zina mwa nkhanzazo n’zomwe apolisi ankachitira anthu akawapeza kopemphera, kumowa kapena akuyenda itadutsa 8 koloko usiku nthawi yomwe idakhazikitsidwa.
A Kadadzera ati apolisi onse omwe akugwira nawo ntchitoyi adaunikiridwa kale za kagwiridwe ka ntchitoyo kuti pasamvekenso nkhanza zosagwirizana ndi malamulo.
Anthu m’mizinda yonse ikuluikulu adasonyeza kuti ayamba kutsatira malamulowo koma ena akadanyozera.
Mwachitsanzo, ku Blantyre Lolemba pomwe opaleshoni imayamba anthu ambiri adayesetsa kuvala masiki komanso magalimoto onyamula anthu adayesetsa kutsata mlingo woyenera.
Mumzinda wa Lilongwe zidayamba mwa kasakaniza pomwe anthu ena amavala masiki pomwe ena amangoyenda ngati kuti kulibe matendawa.
Galimoto zonyamula anthu nazo kufikira mpaka Lachitatu zimangonyamulapo bola anthu apezeka ndipo eni galimotozo samalabada kuti anthuwo avala masiki kapena ayi.
Mneneri wapolisi m’chigawo chapakati a Alfred Chimthere adatsimikiza Lolemba kuti aonetsetsa kuti apolisi ali ponseponse kuonetsetsa kuti malamulo a Covid-19 akutsatidwa.
“Tidaunika kale ndipo ndondomeko ili mmalo kwatsala timwaze asilikali anthu kuti anthu ayambe kutsatira zomwe malamulo akunena. Wonyozera n’zawo chifukwa chenjezo lidaperekedwa kale, azilipira chindapusa,” adatero a Chimthere.
Ku Mzuzu ndiko opaleshoni idayamba mozizira kwambiri chifukwa zovala masiki kapena kunyamula mlingo oyenera m’magalimoto kudalibe Lolemba.