Nkhani

Othawa madzi ati bola azibwerera kwao

Listen to this article

Mawu oti kwanu n’kwanu m’thengo mudalaka njoka lero akupherezeka pomwe anthu ena amene adathawa madzi osefukira kumunsi kwa chigwa cha Shire, maka ku Nsanje, akuti akufuna boma liwalole azibwerera kwawo ponena kuti ndi bwino akavutike kusowa pogona koma azikalima.

Nyakwawa Katandika ya kwa T/A Nyachikadza yomwe ikusungidwa pamsasa wa Bitilinyu m’bomalo, yati iyo ndi anthu ake akuopa kuti ngati sabwerera msanga ndiye kuti sakhala ndi mwayi wolima, zomwe zingawabweretsere njala yoopsa chaka chino mpaka chamawa.

floods2“Anzathu chimanga chikupota, pamene ife sitidayambe ndi kulima komwe. Mvula sichedwa kusiya kuno. Ngati tingokhala m’misasamu, ndiye kuti tikuputa dala njala,” Katandika adauza Tamvani Lachiwiri.

Koma mkulu woona zomangamanga kuofesi ya DC wa Nsanje, Kennedy Adamson, wanenetsa kuti ngati anthuwo akufuna kupita kapena akukakamirabe m’malo angoziwa ndiye sapeza nawo mwayi wa nyumba zotsika mtengo.

“Boma limanga nyumba zotsika mtengo m’madera amene simukhudzidwa ndi ngozizi. Ndiye ngati ena akukana kusamukira kumtunda kapena akubwerera [m’malo momwe chaka ndi chaka mukhala vuto la kusefukira kwa madzi], sapindula nawo ndi ndondomekoyi,” adatero Adamson.

Koma Humphrey Magalasi, amene akuyang’anira msasa wa Bitilinyu, akuti ngakhale anthuwa akukakamira kubwerera, pali mantha kuti angakavutike chifukwa madzi sadaphwerebe.

“Kodi akuti apita kuti? Kuli madzi okhaokhatu komwe amakhalako. Ngati panopa tidakasakabe kuti tipeze anthu amene tikuwaganizira kuti adapita ndi ndipo sadapezekebe, ndiye kuti zinthu zili bwino kumeneko?,” adatero Magalasi.

Nawo azanyengo achenjeza kuti kugwa mvula yoopsa kuyambira Lachinayi lathali ndipo pali chiyembekezo kuti ku Chikwawa ndi ku Nsanje madzi asefukiranso.

Mneneri wa nthambi yoona zanyengo Elina Kululanga wati maboma a Blantyre, Zomba ndi Mulanje ndiwo ali pachiopsezo cholandira mvula yochuluka.

“Ikhala yaziphaliwali komanso yamphepo ya mkuntho. Ndi mvula yambiri, chiyembekezo chilipo kuti kuchigwa cha Shire madzi asefukiranso,” adatero Kululanga ouza Tamvani Lachiwiri.

Kodi nyakwawa Katandika akuti chiyani pa zomwe odziwa zanyengo akunenazi?

Iyo ikufotokoza: “Chadutsa chija ndi chinyama, sizingatheke kuti madzi otere adutsenso. Ineyo chibadwireni sikunadutseko madzi ngati amenewa. Tisaope, madzi amene aja apita. Malo olima alipo, tikalima kumtunda chifukwatu madziwa aphwerako kusiyana ndi momwe timachokako.”

Kwa maola awiri amene Tamvani idakhala pamsasa wa Bitilinyu womwe ukusunga anthu oposa 3 000, nkhani yomwe anthu ambiri amakamba ndi yoti abwerere kwawo basi.

Ngakhale zakudya zikubwera pamsasawu, anthuwa akuti sakukondwa ndi momwe akuwagawira chakudyacho.

“Tikuyenera tizidya katatu patsiku, koma tikumadya kawiri basi, komanso chakudya chake chochepa. Kodi ngati sitilima ndiye tizivutikabe chonchi?

“Boma litipatse mapepala apulasitiki kuti tikamangire nyumba ndipo litivomereze kubwerera kwathu,” idatero mfumuyi yomwe idatinso mudzi wake wonse udathawa madzi oopsawo.

Izinso zili chonchi ndi kumsasa wa Makhanga ndi ku Osiyana m’bomalo komwe, malinga ndi mkulu wa zaulimi Isaac Ali, anthu ena ayamba kale kutuluka m’misasa yawo.

“Ndauzidwa kuti anthu ena akwezedwa mabwato ndipo abwerera. Akuti akukhala cha ku Khonjeni mbali ya Thyolo komwe kulibe chakudya. Kupitako n’kovuta chifukwa cha mayendedwe,” adatero Ali.

Mvula ya mphamvu idagwa kumayambiriro a mwezi uno ndipo maboma a Chikwawa, Nsanje, Phalombe, Zomba, Rumphi, Karonga, Thyolo, Machinga, Mangochi, Ntcheu, Chiradzulu, Mulanje, Balaka, Salima ndi Blantyre ndiwo adakhudzidwa.

Malinga ndi zomwe mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika walankhula Lachiwiri lapitali, anthu 174 000 atsamutsidwa m’malo mwawo kaamba koti nyumba zawo zakokoloka ndi madzi.

Iye adati sukulu 234 zagwetsedwa ndipo sukulu 181 ndizo zikugwiritsidwa ntchito ngati malo othawirako.

Mutharika adati chiyambireni mavutowa, boma lake lakhala kalikiriki kuthandiza anthu amene akhudzidwawa ndipo ndalama zoposa K38 biliyoni ndizo zikufunika kuti zithangate anthuwa.

 

Related Articles

Back to top button