Pali mtsutso pa zotsegulira sukulu
Pomwe unduna wa zamaphunziro watsindika kuti ophunzira a m’sukulu zogonera komweko akuunikidwa zizindikiro za Corona akafika, bungwe la aphunzitsi la Teachers Union of Malawi (TUM) lakana kuti izi sizikuchitika.
Tamvani adali ndi chidwi kulondoloza ngati zomwe unduzawo adalonjeza potsekera telemu yachiwiri kuti potsegulira telemu yachitatu ophunzira m’sukulu zogonera komweko adzayenera kuunikidwa polowa mumpanda zikuchitika.
Mlembi wamkulu wa unduna wa zamaphunziro a Chikondano Mussa Lachitatu adati zinthu zikuyenda bwino m’sukulu ndipo mwana aliyense akuunikidwa pofika pasukulu.
“Ndinganene kuti zinthu zayamba bwino ndipo kuunika kukuchitika koma pakalipano tilibe nambala yeniyeni kuti taunika angati ndipo zotsatira zikutuluka zotani. Koma omwe akupezeka ndi zizindikiro tikuwaika pamphepete kuti akayesedwe bwinobwino,” adatsimikiza a Mussa.
Koma Lachitatu lomwelo, mkulu wa bungwe la TUM a Willie Malimba adati ili ndi bodza la mkunkhuniza chifukwa konse komwe bungwelo layendera, mumpanda osayesedwa.ophunzira akungolowa
“Akunama zimenezo sizikuchitika nkomwe ayi, ngakhale inuyo mutati muyendere sukulu zingapo m’zigawo zonse mutsimikiza chifukwa tisamapakane mafuta pakamwa ayi,” adatero a Malimba.
Kadaulo pa zamaphunziro a Benedicto Kondowe adati kusemphana maganizoku kukuyenera kukhalapo chifukwa olo kuunika kutakhalapo sizingafanane m’sukulu zonse.
“Nkhani yoyamba ndi mapezedwe a sukulu iliyonse komanso boma limapereka zipangizo mosiyana m’sukulu malingana ndi sukuluyo ndiye zambiri zayenera kusiyana,” adatero a Kondowe.
Nkhawa ina ya a Malimba ndiyazipangizo zodzitetezera komanso zaukhondo zomwe akuti mpaka pano sizidagulidwe m’sukulu zambiri komanso sukulu zambiri zatsegulidwa osapopera mankhwala ngati momwe zidakhalira telemu yatha.
“Boma lidapereka K100 miliyoni m’boma lililonse kudzera kumawofese a zamaphunziro koma tikudabwa kuti mpaka pano zipangizo sizikugulidwa. Aphunzitsitu ali pachiopsezo kwambiri,” adatero a Malimba.
Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe okjudzidwa ndi zaumoyo wa Malawi Health Equity Network (Mhen) a George Jobe adati mpofunika kusamala makamaka potanthauzira kuunika ndi kuyesa Covid-19 komanso kuti akati zodzitezera kwa aphunzitsi n’chiyani.
“Pali nkhani ziwiri apapa, yoyamba ndi yoti kodi kuunika Corona nchiyani nanga aphunzitsi akati akufuna zodzitetezera akunena chiyani chifukwa zodzitetezera ndi dzina la gulu.
“Aphunzitsiwo abwere poyera kuti akufuna masiki, sopo, ziwiya zosambira mmanja ndi sanitayiza kuti bajeti yawo isavute komanso isaoneke yaikulu ayi,” adatero a Jobe.
Koma a Malimba adati boma lipereke ndondomeko yakagulidwe ka zipangizozo kwa akuluakulu amaphunziro m’maboma nthawi isadathe chifukwa mayeso a Sitandade 8 ayandikira ndipo kudziteteza kudzafunika kwambiri panthawiyo.
A Mussa ati unduna wawo utulutsa zotsatira za kuunika komwe akuti kukuchitika akamaliza kutolera za mmaboma onse.