Sitinadye mabanzi
Archbishop wa mpingo wa Katolika a Thomas Msusa atsutsa zoti maepikisikopi a mpingowo sakulankhula kanthu pa mavuto omwe Amalawi akukumana nawo kaamba koti adya mabanzi (adalandira ziphuphu).
A Msusa adalankhula izi pa misa yomwe adachititsa pa mpingo wa St Anthony m’mzinda wa Blantyre.

A Archbishop amathirirapo ndemanga pa zomwe Akatolika ena akunena zoti maepisikopiwo alandira ziphuphu n’chifukwa chake sadzudzula boma pa mavuto omwe Amalawi akukumana nawo.
Iwo adati Amalawi azidzilankhulira okha akamva kupweteka m’malo modikira maepisikopiwo kuti alembe kalata.
A Msusa adati n’kulakwa kuloza zala maepisikopiwo kuti adya mabanzi pomwe Amalawi eni ake sakufuna kulankhula pa okha.
“Aliyense wobatizidwa adalandira mphatso yauneneri choncho akhoza kulankhula akaona zolakwika.
“Ngati maepisikopi nthawi yathu ikakwana, tilemba kalata yofotokoza momwe zinthu zilili m’dziko muno,” iwo adatero.
A Msusa adafunsa kuti ngati ndalama zakunja zikuvuta, nanga ogulitsa galimoto akuzipeza kuti?
“Kodi a bizinesi yogulitsa galimoto akupeza kuti ndalama zakunja zogulira galimoto pamene boma likukanika kugula mafuta kaamba kosowa kwa ndalamazo?
“Ngati m’zipatala za boma mulibe mankhwala kaamba koti ndalama zakunja zikusowa, nanga zipatala za anthu ndi mabungwe akugula bwanji mankhwala awo?” Adafunsa a Arcbishop.
Iwo adati Amalawi akudzionera okha koma salankhula kapena kuchitapo kanthu.
Anthu ambiri akugona pa mizere ya mafuta kaamba ka vuto la mafuta lomwe lagwa m’dziko muno. Boma likuti vutoli ladza kaamba ka kusowa kwa ndalama zakunja.
Mwezi wathawu mkulu wa Malawi Conference of Catholic Bishops a Martin Mtumbuka adadzudzula atsogoleri a dziko lino ati kaamba ka kuthimathima kwa magetsi komanso chifukwa cholowerera pa kayendetsedwe ka makampani a boma.
Amalawi adazolowera kuti maepisikopi a Katolika amalemba kalata yofotokoza momwe ndale ndi chuma cha dziko lino zikuyendera.
M’chaka cha 2025, maepisikopi a Katolika adalemba kalata kutangotsala nthawi pang’ono kuti Amalawi akaponye mavoti a pa 16 September 2025 younikira anthu momwe zinthu zidaliri m’dziko muno.
Kalatayo idauza anthu kuti akavotere atsogoleri abwino, woona mtima, olimba mtima komanso omwe ali ndi mtima wofuna kuthana ndi mavuto awo.
Pa 6 March 1992 maepisikopi a mpingo wa Katolika adatulutsa kalata yomwe idathandizira kusintha ndale za m’dziko muno.
Posachedwapa, mpingo wa CCAP mu sinodi ya Livingstonia udapempha boma kuti lichepetse mavuto omwe anthu akukumana nawo m’dziko muno.



