Chichewa

‘Takulira limodzi, kuchokera ubwana’

Listen to this article

 Lucius Banda adaimba nyimbo yomwe imati: Takulira limodzi, kuyambira ubwana…. Kusiyana kwake n’koti anthu amaimbidwa m’nyimboyo mapeto sadakwatirane. Si zili choncho ndi achikondi awiri amene zonse zidakathera m’banja.

Geoffrey Chanza ndi Getrude Ghambi adakumana ali achichepere. Iwowa akula limodzi ku Engucwini m’boma la Mzimba komwenso amapemphera mpingo umodzi.

Panthawiyi awiriwo akuti amangodziwana ngati anthu basi koma panalibe chilichonse pakati pawo komanso samachezerana.

Koma zinthu zinasintha 2016 Getrude akuchita maphunziro ake a unamwino m’chaka choyamba.

Geoffrey and Getrude tsiku la ukwati wawo

“Tidakumana patsamba la m’chezo la Facebook n’kuyamba kucheza. Tinapatsana manambala n’kumacheza pa Whatsapp,” adatero iye.

Malinga ndi Gertrude awiriwo adakumananso ku Mzuzu panthawi ya tchuthi.

“Geoffrey anandiuza mawu kuti wakhala akundifuna koma amaopa kundiuza. Ndinamuyankha kuti andipatse nthawi chifukwa ine ndinkamutenga ngati mnzanga ndipo sindinkachimva mkati mwanga,” anatero Getrude.

Koma pofika 2018, chibwenzi cha awiriwo chinayamba.

“Patadutsa miyezi yochepa, tinadzasiyananso chifukwa cha nkhani zina ndi zina. Koma patadutsa miyezi itatu tinabwererana,” anatero Getrude.

Awiriwo anakhala zaka zitatu pa ubwenzi. Ndipo pa December 11, 2021 anadalitsa ukwati wawo pa St Augustine Catholic mumzinda wa Mzuzu.

Iwo akulangiza anthu omwe akufuna banja kuti adekhe ndi kudikira pa Mulungu.

Iwo adatinso mavuto omwe amakumana nawo ambiri amathana nawo powapereka m’manja mwa Mulungu.

Getrude ndi namwino komanso mzamba pachipatala cha boma ku Nkhata Bay pomwe Geoffrey amagwira ntchito ku Vision Fund.

Awiriwo akukhala m’boma la Nkhata Ba

Related Articles

Back to top button
Translate »