Chichewa

The Rain: Mnyamata wanthetemya

Listen to this article

 

Anthu ambiri otchuka makamaka amasewero, oyimba ndi azisudzo amakonda kudzitcha maina otchukira kusiya awo a pamchombo. Mchitidwewu sudayambire kuno ku Malawi, ayi, koma ngakhalenso kumaiko akunja ziliko. Tikakamba za kwathu kuno tili nawo maulendo a Soldier, Anong’a, Piksy, Shakira, Safintra ndi ena. Omwe atchulidwa apawa ndi zitsanzo chabe koma alipo ambiri makamaka achinyamata omwe akutchuka ndi nyimbo zamakonowa. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Bright Vitsotso, mnyamata yemwe watchuka pawailesi ndi kanema ndi nyimbo zamakono ndipo iye akuti dzina lake lodyera ndi ‘The Rain’.

Vitsotso: Ndimagawa nthawi yanga
Vitsotso: Ndimagawa nthawi yanga

Tandifotokozera kuti ndiwe ndani mnyamata.

Dzina langa ndi Bright Vitsotso wa kwa Waliranji m’boma la Mchinji, koma ndikukhala ku Lilongwe.

 

Wati Bright Vitsotso, nanga ‘The Rain’ akuchoka pati?

‘The Rain’ ndi dzina lomwe ndimatchuka nalo pazoimbaimba. Pali maina awiri la ‘The Rain’ ndi ‘Young Star’ omwe anthu otsata nyimbo zanga amadziwa.

 

Umaimba chamba chanji?

Ndimaphatikiza Rap ndi Hip Hop zomwe ndimaziimba motsatira mingoli ya Chifirika. Panopa ndidapanga chikole ndi kampani yojambula nyimbo ya Dash Travellers Entertainment ndipo ndikugwira nawo bwino kwambiri ntchitoyi.

 

Luso lako lidayamba liti?

Chilakolako choimba chidandiyamba m’chaka cha 2005 pomwe ndinkaimba ndi anzanga koma zidali ngati zamasewera chabe. Ndikukula ndidayamba kulemba nyimbo zokhudza zinthu zochitikadi m’moyo wa munthu n’kumayeserera kuziimba uku ndikudzijambula ndekha n’kuona kuti zikumveka bwino ndithu.

 

Pakalipano uli ndi nyimbo zingati?

Ndili ndi nyimbo zingapo, yoyamba kujambula idali Chikumbuntima yomwendidathandizana ndi Peter Banda ndi Mabilinganya Empire. Kenako ndidajambula Swazi ndi Mabilinganya Empire kenako Honey yomwe ndidajambula ndi Katelele Ching’oma. Nditangomaliza imeneyi ndidajambula Ndikuopa ndi Lady Pace n’kupuma kaye.

 

Nyimbo zako zimakhala ndi uthenga wanji?

Nyimbo zanga zimakamba za mmene moyo ulili ndi nkhani zochitikadi. Sindifuna kuimba nyimbo zokhala ngati nthano, ayi, koma zoti munthu akamamvera azitha kulumikiza zomwe ndikunena ndi zomwe amakuna nazo kapena kuona m’moyo.

 

Kupatula zoimba, china chomwe umachita ndi chiyani?

Kupatula kuimba ndimalembanso mafilimu, kuvina, kusewera mpira komanso ndidapanga za magetsi ku Yunivesite ya Nairobi ku Kenya kenako ndidagwirapo ntchito m’mapolojekiti a Airtel kwa zaka 5 koma pano ndikupitiriza maphunziro ku United Arab Emirates.

 

Ukuoneka wotangwanika, ndiye zonsezi umakwanitsa bwa?

Ndimagawa nthawi yanga bwinobwino moti kundipeza ndikungokhala si kwenikweni ayi. Ndikathana ndi zakuntchito ndimapita pazida zanga n’kumapanga za nyimbo. Sindifuna kungotaya nthawi yanga.n

Related Articles

Back to top button
Translate »