Nkhani

Tom sakufunanso ndalama?

Listen to this article

Kati deru kadazizwitsa mlenje. Ife aganyu tadzidzimuka ndi ganizo la mphunzitsi wa Flames Tom Saintfiet yemwe tsopano wanena kuti sakufunanso K3.3 miliyoni akakapuntha Nigeria pa 7 September.

Ife tidayamba kutolera za m’mageti kuti pofika pa 7 zikhale zitakwana koma lero kudzidzimuka akuti ndalama ayi. Ah ah ah! Zataninso wawa?

Pamene Uncle Tom amabwera adagwirizana ndi Fam kuti iwo abwera ngati mfalisi ndipo ntchito yawo ndiyokagwetsa Nigeria. Komabe Uncle Tom adalamula Fam kuti idzawapatse K3.3 miliyoni lotolo akalichenutsa.

Lero Uncle Tom asintha maganizo, akuti iwo ndalama si nkhani ndipo ngakhale akatsotsomole Nigeria Fam isadzawapatsenso ndalamazo.

Kodi pamene Uncle Tom amalamula ndalamazo samadziwa kuti iwo ndi andalama kale? Kapena mwadziwa kuti Fam imaphangirana ndi matimu potolera za pageti zomwe zingatenge nthawi kuti ndalamayo ikwane? Kapena mwazindikira kuti chitunda chimenechi sitingakakwerepo?

Monga mwa mawu anu, aganyu sitikukayika kuti pa Nigeria tikadutsapo ngakhale mphunzitsi wa Nigeria wadzipereka kusiya ntchito yake akakagonja ndi Flames.

Mwina osewera athu atengerepo phunziro kuti si bwino kumasewera ndi mtima wofuna kulandira kanthu koma mmalo mwake kufuna kupanga mbiri. Kukagwetsa Nigeria kwawo ndi nkhani yomwe ingatekese dziko lapansi. Izi zikutitsimikizira kuti ngakhale popanda malonjezano inu mukangogwira ntchitoyo.

Related Articles

Back to top button