Nkhani

Za mahedifoni pamsewu

Listen to this article

Malinga ndi kupita patsogolo kwa zipangizo zogwiritsa ntchito pamoyo wa tsiku ndi tsiku, makhalidwe ndi zochita za anthu zikusinthanso.

Pafupifupi aliyense ali ndi foni ya mmanja ndipo achinyamata ambiri ali ndi zida zanyimbo zomwe akamayenda amakhala akumvetsera pogwiritsa ntchito mahedifoni.

Kumvetsera nyimbo kumathandiza kuti munthu usasungulumwe, kungoti nthawi zina timakhala ngati sitimakaganizira bwino kagwiritsidwe ntchito ka zidazi, makamaka tikakhala pamsewu.

Masiku ano umatha kupeza munthu akuyendetsa njinga pakati pamsewu mahedifoni ali m’khutu; kotero kuti kaya dalaivala aimbe bwanji hutala, wapanjinga samamva chifukwa cha nyimbo zomwe akumvetsera.

Madalaivala enanso a minibasi ndi galimoto zina amagundika kukweza nyimbo za mahedifoni ali pamsewu, posaganizira kuti akusokoneza ntchito yomwe makutu amayenera kugwira posamala kayendedwe ka pamsewu komanso moyo wawo ndi miyoyo ya anthu ena omwe akugwiritsa ntchito msewuwo.

Aliponso ena oyenda pansi omwe akalonga mahedifoni m’khutu amangodziyendera pamsewu mwamgwazo osalabadira zomwe zikuchitika.

Choncho amapezeka kuti akuyenda pakati pamsewu kapena kuoloka nthawi yolakwikwa chonsecho makutu atseka ndipo sakumva chilichonse.

Khutu ndi chimodzi mwa ziwalo zomwe oyendetsa galimoto komanso oyenda pansi amayenera kugwiritsa ntchito pamsewu kuti amvane komanso kupewa ngozi, choncho zingathandize kuti makutuwa adzipatsidwa mpata kuti agwire ntchito yake pamsewu.

Ngakhale mahedifoni amathandiza kusangalatsa munthu akakhala yekha kapena akamayenda mtunda wautali, kupanda kuwagwiritsa ntchito mwa nzeru angachititse ngozi zomwe zikadatha kupeweka.

Pamsewu pamachitika zambiri ndipo pamakhala anthu osiyanasiyana—ena amgwazo, ena achangu, ena oledzera—choncho nkofunika kuti munthu ukamayenda nzeru zonse zizikhala pamsewupo mmalo momamvera nyimbo utasiira ena udindo wosamalira moyo wako.

Related Articles

Back to top button