Nkhani

Ukaidi kwa bambo, mayi pa zogwirira mwana

Anthuwo ndi banja. Koma lero lino laima kaye. Mwamuna akukaseweza kundende zaka 21. Mkazi wake apita kozizirako zaka 5.

Masiku osiyana, bwalo la majisitileti m’bomalo lidapeza bamboyo, (yemwe sitimutchula dzina) wa zaka 41, wolakwa pogona ndi mwana wake womupeza wa zaka 14. Mayiyo, (yemwenso sitimutchula dzina) wa zaka 33, akagwira ntchito ya kalavula gaga kaamba kolola mwamuna wakeyo kugona ndi mwana wakeyo, yemwe adamupeza kubanja lake loyamba.

Bwalo la milandu ku Mangochi lagamula kuti ana atatu a pabanjalo azithandizidwa ndi nthambi ya zosamalira anthu m’boma la Mangochi.

Bamboyo adaphwanya Gawo 138 la malamulo a dziko linno pogona ndi mwana wamng’ono, pomwe mkazi wakeyo adaphwanya Gawo 142 pothandizira kuti izi zichitike.

Bwalolo lidamva kupyolera kwa wapolisi a Amos Mwase kuti mayiyo adatseketsa koma ali ndi ana atatu kuchokera kubanja lake loyamba ndipo mwana wogwiriridwayo ndi chisamba.

“Kuyambira mwezi wa April mpaka July chaka chino bamboyo adakhala akugona ndi mwanayo, nthawi zinanso mayi wake akuona,” adatero a Mwase.

Koma atatopa ndi mchitidwewu, pa 8 July, mwanayo adakamang’ala kwa agulupu a Ching’anda omwe adakanena kupolisi ya Makanjira. Kuchoka apo adapita kuchipatala chaching’ono cha Makanjira komwe adamuyeza ndipo kudapezekadi kuti adamugwirira.

Koma m’bwalo la milandulo, mayiyo adaukana mlanduwo zimene zidachititsa kuti apolisi abweretse mboni zitatu.

Bamboyo adapempha bwalolo kuti liwapatse chilango chofewa chifukwa ana awo avutika iwo akapita kundende chifukwa akhala opanda owasamala. Koma a Mwase adati bwalo lisamvere izo chifukwa sadakwanitse ntchito yawo ngati kholo kuteteza mwana wawo.

Ndipo mwamuna wawo adapempha bwalolo kuti liwachitire chifundo chifukwa aka kadali koyamba kupalamula mpaka kubwalo. Iwo adapepesa.

Poweruza, Michongwe adati ukaidi uchititsa ena a maganizo otere kuti apewe kutero. Iye adalamula ofesi ya chisamaliro cha anthu m’boma la Mangochi kuti asamalire anawo.

Ndipo podzudzula khalidwe la abambo ogona ndi achichepere limene lakula, mmodzi mwa akadaulo oona zoti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo pantchito a Emma Kaliya adakhutira ndi chilango chimene chidaperekedwa.

Polankhula ndi mtolankhani wathu, a Kaliya adati zimene adachita mayiyo n’zochititsa manyazi ndipo adayamikira woweruza Rodrick Michongwe popereka chilango chotere kuti amayi ena amene angakhale ndi maganizo otere atengerepo phunziro.

“Amayi ambiri akuchita zimenezi pofuna kuteteza mabanja koma amaiwala kuti akuphwanya ufulu wa mwana. Ndiyamikire mwanayo poulula chifukwa naye watsegula njira kwa anzake ena omwe akufera mkatikati. Amfumu nawo ndi anzeru kwambiri chifukwa ena amanyengereredwa n’zazing’ono,” atero a Kaliya.

Iwo adati akadakondanso mlanduwo ukadapita khoti lapamwamba kuti zilango za makolo awiriwo zikakwere.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button