Nkhani

Womukaikira zopakula ku Kapitolo adzipereka

Listen to this article
Adakali ku South Africa: Mphwiyo
Adakali ku South Africa: Mphwiyo

Wabizinesi Osward Lutepo, amene wakhala akusakidwa ndi apolisi a dziko lino, komanso polisi ya maiko osiyanasiyana ya Interpol, Lachitatu adatera m’dziko muno kuchokera kunja ndipo adakadzipereka kulikulu la polisi ku Area 30 mumzinda wa Lilongwe.

Lutepo, yemwenso ndi mmodzi mwa akuluakulu a chipani cholamula cha People’s Party (PP), akumuganizira kuti amagwirizana ndi ogwira ntchito m’boma ena kuti azipakula ndalama zaboma kupyolera m’makampani ake amene amalandira mamiliyoni ochuluka koma osagwira ntchito iliyonse.

Padakalipano, anthu oposa 20 akhala akukaonekera kukhoti pokhudzidwa ndi kusowa kwa mabiliyoni a boma. Ena mwa iwo amagwidwa ndi mamiliyoni osaneneka kumabuti a galimoto ngakhalenso m’nyumba zawo, ndalama zimene akuganiza kuti zimasololedwa kunjira yolipirira pantchito ndi katundu yemwe boma limagula ya Integrated Financial Management System (Ifmis).

Chongofika m’dziko muno, Lutepo adapita kupolisi motsagana ndi womuimira pamlanduwo, Jai Banda.

Wachiwiri kwa mneneri wa likulu lapolisi Kelvin Maigwa adati Lutepo, yemwe ndi wa zaka 35, adakadzipereka yekha.

“Tili naye ndipo tikumufunsa mafunso angapo. Padakalipano, milandu imene timuzenge sinadziwike,” adatero Maigwa.

Bungwe lothana ndi ziphuphu la Anti-Corruption Bureau (ACB) lidatseka mabuku akubanki a makampani 20 amene akuwakaikira kuti akukhudzidwa ndi chipwirikiti chopakula mabiliyoni a boma. Makampani 8 adali a Lutepo, kapena amene amayendetsa mogwirizana ndi anthu ena.

Izi zili choncho, Pika Manondo, mkulu wina amenenso akusakidwa ndi apolisi pomuganizira kuti akukhudzidwa ndi mlandu wofuna kupha mkulu woonetsetsa kuti ndondomeko ya chuma cha boma ikuyendetsedwa bwino, Paul Mphwiyo, adauza nyuzipepa ya The Nation kuti abwera m’dziko muno pofika mawa.

Iye adati ndi wokonzeka kuthandiza apolisi pazofufuza zawo zokhudza kuomberedwakwa  Mphwiyo pa September 13, 2013 pomwe amati azilowa pachipata cha nyumba yake ku Area 23. Nthawiyo n’kuti Mphwiyo atagwira ntchitoyo kwa miyezi iwiri.

Apolisi adanjata MacDonald Kumwembe yemwe adakhalapo msirikali, komanso Robert Kalua powaganizira kuti ndiwo adaombera Mphwiyo. Apolisiwo adagwiranso Dauka Manondo, mng’ono wake wa Pika.

Kupakula kwa ndalama kwakhudza kwambiri boma la mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda, yemwe sabata zapitazo adachotsa nduna zake zina, kuphatikizapo yemwe adali nduna ya zachuma Ken Lipenga ndi yemwe adali nduna ya za malamulo Ralph Kasambara.

Ndipo apolisi sabata yatha adakachita chipikisheni kunyumba kwa Kasambara, kuyang’ana galimoto imene akuti idagwiritsidwa ntchito pokaombera Mphwiyo, yemwe akadali ku South Africa ngakhale adatuluka kuchipatala kumene amalandira thandizo.

Related Articles

Back to top button
Translate »