‘Zionetsero zili m’njira’

Mgwirizano wa mabungwe omenyera ufulu wa anthu wa Human Rights Defenders Coalition (HRDC) wati ukukonza mchochombe wina wa zionetsero zofuna kuthotha wapampando wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC), Jane Ansah.

Zionetserozi zidachita mpumuliro kwa mwezi watunthu pomwe akuluakulu a HRDC adali kunja kokagwira ntchito zina.

Pa zionetsero za mmbuyomu, anthu adaotcha galimoto la polisi

Akuluakuluwa afika m’dziko muno sabata yatha ndipo wachiwiri kwa wapampando wa HRDC Gift Trapence wauza Tamvani kuti tsopano Amalawi avale zilimbe chifukwa zionetsero zafikanso ndipo zikhala za motomoto.

“Pa mwezi umenewu, talandira mafunso ambiri okhudza zionetsero ndipo ena amaona ngati tidagwa mphwayi kapena tidameza chibanzi koma ayi ndithu, anthu ake siife opanga zimenezo. Tabwera ndipo kukhala zionetsero zakathithi,” adatero Trapence.

Ndipo katswiri pa ndale George Phiri wati mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika komanso Ansah akadapaga zinthu zothandiza dziko pogonjera zofuna za anthu chifukwa zionetsero zomwe zingapangike tsopano zikhoza kusakanikira ndi mkwiyo wa zomwe anthu achitiridwa.

“Pali zambiri zomwe anthu zikuwapweteka monga nkhanza zomwe  zidachitika kwa Msundwe, anthu ambiri avulazidwa ena mpaka kuphedwa m’madera osiyanasiyana koma boma osaonetsa kulabadira kulikonse, zina ndi izi zikumveka zogulitsa malozi komanso chichitikire zionetsero zoyamba, palibe yankho lililonse,” adatero Phiri.

Amalawi ena, motsogozedwa ndi HRDC, akufuna kuthotha Ansah pomuganizira kuti sadayendetse bwino chisankho ndipo nkhani iyi ikufananako ndi yomwe atsogoleri a Malawi Congress Party (MCP) Lazarus Chakwera komanso Saulos Chilima wa UTM Party akufuna kuti khoti ligamule kuti chisankho sichidayende mwachilungamo ndipo chichitikenso.

Pamene mlanduwo ukuyembekezeka kulowanso m’khoti pa 25 November, ofesi ya kazembe wa ku Mangalande idapempha atsogoleri azipani kuti akonzekeretse anthu awo kudzavomereza zotsatira.

Kadaulo pa zakayendetsedwe kwa zinthu m’dziko, Makhumbo Muthali, wati zionetsero za HRDC zipitirire chifukwa sizikukhudzana n’komwe ndi za nkhani ya kukhoti ndipo chenjezo la ofesi ya kazembe wa ku Mangalande likukhudza za kukhoti osati zionetsero.

“Chofunika, zipani ziuze anthu awo kuti azitsatira momwe nkhani ikuyendera kukhoti akatero sipadzakhala povuta kuvomereza koma kuti anthu asapange zionetsero polingalira kuti mwina zingadzakolezere upandu, sizoona. Anthu agwiritse ntchito ufulu wawo,” watero Muthali.

Ndipo polankhula masiku apitawa, mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adadzudzula zionetsero ponena kuti zimangobwezeretsa chitukuko mmbuyo ndipo n’zosayenera.

Poyankhapo, Munthali adati kulakwa kwakukulu kwa Mutharika n’kusafuna kumva zonena za Amalawi. Iye adati anthu sakukondwa ndi momwe chuma chikuyendera, kusatsata malamulo komanso ndale zosayenda.

“Vuto la Mutharika akungoona ngati zionetsero zikuthera pa Ansah koma pali nkhani zambirimbiri mkatimu zomwe atazimva n’kuzikonza zionetsero zikhoza kutha pomwepo,” adatero Munthali.

Woyendetsa ntchito za bungwe la Chikatolika loona za mtendere ndi chilungamo (CCJP) Boniface Chibwana wati ofesi ya kazembe wa ku Mangalande idanena mfundo yabwino chifukwa zovuta zingakule bwanji, mapeto ake ofunika ndi mtendere ndi chilungamo.

Iye wati ngakhale atsogoleriwo akufunika kumvera malangizowa, palibe chifukwa choletsera anthu kupanga zionetsero chifukwa ndi ufulu wawo kutero. Chofunika, iye adati, n’kutsatira malamulo basi komanso atatsatira ndondomeko yoyenera.

“Ufulu wa anthu, mtendere ndi chilungamo n’zofunika kwambiri ndiye zipani ziyendetse mlandu wawo kukhothi, mbali inayi, anthu agwiritse ntchito ufulu wawo omwe uli mmalamulo,” watero Chibwana.

Koma mneneri wapolisi James Kadadzera wati sayankhapo msanga pankhaniyi ku mbali yachitetezo mpaka alumikizane ndi akuluakulu ena kupolisi.

Zionetsero za mtundu omwewu zomwe HRDC imatsogolera chitangochitika chisankho pa 21 May 2019, zinthu zambiri zidawonongedwa, kubedwa ndipo anthu ena adavulazidwa mpaka mnyamata mmodzi wochokera ku Karonga adamwalira.

Share This Post