Zipani zakonzeka kusankha makomishona
Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika wauza zipani za ndale komanso nthambi yoyang’anira ogwira ntchito makhoti (Judicial Service Commission) kuti apereke maina a omwe akuona kuti akhonza kukhala makomishona a bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) komanso wapampando wake.
Izi zikutsatira kutula pansi mpando kwa yemwe adali wapampando wa bungwe la MEC Jane Ansah komanso polingalira kuti mphamvu za makomishona ena onse zikutha pa 5 June 2020.
Malingana ndi mneneri wa Mutharika, Mgeme Kalilani, mtsogoleri wa dziko linoyo wapanga izi pofuna kuti kubungwe la MEC kusakhale mphako mphamvu za makomishona enawo zikatha.
“Apulezidenti sadapereka nthawi yeniyeni yoti mainawo abwere koma polingalira kuti tikuthamangitsana ndi nthawi yachisankho cha Pulezidenti, tikuyembekeza kuti zipani komanso amakhoti apereka msanga mainawo,” adatero Kalilani.
Malingana ndi malamulo, wapampando wa MEC amasankhidwa ndi komiti ya makhotiyo ndipo mneneri wa nthambi ya makhoti Agness Patemba watsimikiza zoti nthambiyo yalandira kalata youzidwa kuti ipereke dzina.
“Kalata yatipeza ndipo komiti ya makhoti ikumana kuti iunike momwe zikhalire koma zikhala zachangu potengera kuti makomishona afunika pachisankho chikudzachi,” adatero Patemba.
Khothi lidagamula pa 3 February 2020 kuti chisankho cha Pulezidenti chichitikenso potsatira umboni omwe udaperekedwa pamlandu woti chisankhocho sichidayende bwino.
Saulos Chilima wa UTM Party ndi Lazarus Chakwera wa MCP ndiwo adakasuma kuti bungwe la MEC lidasokoneza chisankho cha pa 21 May 2019 litalengeza kuti Peter Mutharika wa DPP ndiye adapambana.
Khothilo lidaperekanso mphamvu ku Nyumba ya Malamulo kuti iunike makomishona ngati ali n’kuthekera kopitiriza ntchito koma nyumbayo idapeza kuti makomishona onse adalakwa pantchito yawo ndipo idawunikira kuti achoke pabwere ena.
Katswiri pa ndale George Phiri wati Mutharika wapanga bwino kupereka mpata kuzipani kuti zipereke maina a makomishona koma wati naye apange machawi akalandira mainawo.
Iye wati uwu ukhonzanso kukhala mwayi poti aphungu a Nyumba ya Malamulo akhala akukumana posachedwa ndiye zikhonza kuchita ubwino kuti makomishonawo akawakambiranetu ku nyumbayo.
“Ngati zangochitika, zakhala bwino chifukwa zipani zikapereka maina pulezidenti n’kuvomereza, Nyumba ya Malamulo ikhala ndi mpata owakambirana isadayalule. Tipha mbalame zingapo ndi mwala umodzi,” adatero Phiri.
Malamulo a zachisankho a 2018 amalola zipani zomwe zili ndi aphungu 10 mwa 100 aliwonse kutanthauza kuti pafupifupi aphungu 19 kupita mtsogolo m’nyumbayo kupeleka maina a makomishona.
Apa zikusonyeza kuti m’nyumbayo, zipani za DPP ndi MCP ndizo zili n’kutuekera kopeleka maina a makomishona a MEC.
Mneneri wa DPP Nicholas Dausi watsimikiza kuti chipanicho chalandira kalata youzidwa kuti chipereke maina a makomishona atsopano.
“Talandira ndipo tipanga momwe a pulezidenti anenera. Tisankha anthu angapo n’kuwaunika kenako n’kusankhapo maina omwe akufunikawo n’kupeleka,” adatero Dausi.
Mneneri wachipani cha MCP Maurice Munthali wati chipani cha MCP chidakonzeka kalekale kusankha makomishona atsopano chifukwa icho chimakanitsitsa kuti makomishona akalewa adzayendetsenso chisankho.
“Tipereka maina mosavuta chifukwa nzomwe takhala tikuyembekeza nthawi yonseyi,” adatero Munthali.