Nkhani

Aphungu aunguza njira zokhaulitsira auve

Listen to this article

Uve wanyanya m’dziko muno koma pano zafika poti wina akalowa nazo kundende!

Nyumba ya Malamulo yati nyansi zamgonagona zomwe zili m’makhonsolo osiyanasiyana zikubweretsa fungo loipa komanso zikuika moyo wa anthu pachiwopsezo.  Mosquito

Pachifukwa ichi, aphungu a ku Nyumbayi agwirizana zoti akambirane zokhazikitsa malamulo omwe azipereka mphamvu zonjata munthu wopezeka akuchita utchisi.

Nkhaniyi idalandiridwa ndi manja awiri ndi aphungu osiyanasiyana phungu wa pakati m’boma la Lilongwe Lobin Lowe ataiyambitsa Lachinayi m’Nyumbayi.

Lowe adati nzokhumudwitsa kuti fungo loipa lili ponseponse m’makhonsolo kaamba koti akuluakulu ake amalephera kuchotsa zinyalala komanso zoipa zochoka m’makampani ndi m’mafakitale zikumathera m’mitsinje.

Iye adati izi zikuchitika kaamba koti palibe lamulo loletsa anthu kuchita uve monga momwe zimakhalira m’maiko ena.

“Vuto ndi loti tilibe malamulo ngati m’maiko a anzathu n’chifukwa chake anthu amangotaya zinyalala chisawawa ngakhale kukodza kumene anthu amangokodza momwe afunira chifukwa palibe chilango chilichonse chomwe angalandire,” adatero Lowe.

Phungu wa ku Mpoto cha ku Madzulo kwa boma la Salima, Jessie Kabwila, adavomereza izi ponena kuti chomvetsa chisoni kwambiri nchakuti akuluakulu ena amaphunziro  awo akuchita nawo uve woterewu.

Iye adati uve wotere kuulekerera ukhoza kusokoneza ntchito zokopa alendo kaamba koti anthu obwera amafuna malo ndi zinthu zaukhondo    kuopa woyandikana nawo nyumba.

“Lipoti loyamba likusonyeza kuti iye adayamba kugonana ndi ana akewo m’chaka cha 2014 kutanthauza kuti wina ali ndi zaka 6 pomwe wina adali ndi zaka 4,” Namwaza adatero.

Chiyambireni zolaulazi, mkuluyo akuti wakhala akuopseza ana akewo kuti asadzayerekeze kutsina khutu aliyense za nkhaniyi. Koma poti amati tsoka chimanga chilinda moto, anawo adatopa ndi uvewo.

Namwaza adati aka si koyamba kuti mkuluyo amveke ndi mbiri yomwa mazira akewo.

Akuti mayi wa anawo, yemwe ndi mkazi wake, adawapezapo mwezi wa October chaka chino akuluwo ali ndi mwana wa zaka 7 akupanga naye zadama, koma banjalo lidakambirana za nkhaniyo ndipo idangofera m’mazira.

“Akutitu atakambirana, bamboyo adapepesa komanso adaopseza mayiyo kuti akadzangoyerekeza kuulula adzamukhaulitsa ndiye chifukwa cha mantha, adakhaladi chete,” adatero Namwaza.

Iye adati koma pa November 22 ndi pomwe oyandikana nawo nyumba adalimbikitsa mayiyo kukanena nkhaniyi kupolisi.

Namwaza adati anawo adapita nawo kuchipatala cha Kasungu komwe adakawayesa ndi kuti akalandire thandizo ngati nkoyenera ndipo apolisi akuyembekezera zotsatira.

Tsiku lomwe mwanayo adakaulula za khalidwe la bamboo akewo ndi lomwe bwalo la milandu la magisitireti mumzinda wa Blantyre lidagamula Eric Aniva, fisi wa ku Nsanje, kuti akagwire ndende zaka ziwiri.

Magulu osiyanasiyana, makamaka omenyera ufulu anthu, sadakondwe ndi chigamulochi ponena kuti ndi chochepa ndipo chosakwanira kuthetsa khalidwe lophwanya ufulu wa amayi ndi asungwana.

Mmodzi mwa omwe adadzudzula chigamulochi ndi mkulu wa bungwe la Malawi Human Rights Resource Centre (MHRRC) Emma Kaliya yemwe adati chigamulochi nchosaopsa kwa abambo akhalidweli.

Mkuluyu amachokera m’mudzi mwa Chiswe, mfumu yaikulu Chikumbu m’boma la Mulanje ndipo apolisi ati adzaonekera kukhothi kafukufuku akatha.

Related Articles

Back to top button
Translate »