Nkhani

Chawomola chipande: Mwa anthu 133 345 olembetsa 25 150 okha avota

Listen to this article

Kwatsala utsi wokha, nsima yapsa, chapakula chipande ndipo pakula mtanda pagwera chipani cha MCP chomwe chateteza mpando wa phungu wa kumadzulo kwa boma la Mchinji ndi kupata makhansala awiri m’chisankho chachibwereza chomwe changothachi.

Lachiwiri lapitali, zipani zinayi mwa zipani 50 zomwe zili m’dziko muno zimalimbirana mpando wa phunguwu ndi makhansala anayi a m’mawodi a Kaliyeka ku Lilongwe, Bunda ku Kasungu, Bembeke ku Dedza ndi Sadzi ku Zomba potsatira imfa za omwe adali m’mipandoyi.

Ansah (C):  Tichita kauni wamphamvu
Ansah (C): Tichita kauni wamphamvu

Powomola zonse Lachitatu, chipani cha MCP chidateteza mpando wa phungu ku Mchinjiko kudzanso kulanda mpando wa khansala wa Kaliyeka womwe udali m’manja mwa chipani cholamula cha DPP ndi mpando wa khansala ku Bembeke womwe udali m’manja mwa woima payekha.

Mwachaje satafuna. Nacho Chipani cha DPP sichidabwereko chabe chifukwa chidapambana mipando ya makhansala m’madera a Sadzi komanso Bunda pomwe zipani za PP ndi UDF sizidaphule kanthu pazisankho zachibwerezazi m’madera onsewa.

Menyani: Zaonetsa kuti MCP ndi chipani champhamvu
Menyani: Zaonetsa kuti MCP ndi chipani champhamvu

Ngakhale anthu osiyanasiyana ayamikira momwe zisankhozi zayendera, bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) ndi akatswiri ena ati kuchepa kwa anthu omwe adaponya voti ndi “utsi wofunika kuunika pomwe ukuchokera”.

Mwa anthu 133 345 omwe amayembekezeka kuponya voti, anthu 25 150 okha ndiwo adavota m’madera onse asanu ndipo  wapampando wa bungwe la MEC, Jane Ansah, adati izi n’zofunika kauni wamphamvu.

“Tikuyenera kubwerera kwa Amalawi kukawafunsa pomwe pali vuto kuti asamabwere mwaunyinji kudzavota ngati momwe amabwerera kumisonkhano ya kampeni,” adatero Ansah.

Kasaila: DPP idachitabe  chamuna
Kasaila: DPP idachitabe chamuna

Katswiri wa zandale kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Boniface Dulani, adati gwelo la vutoli ndi khalidwe la andale omwe amaonetsa chibale nthawi ya kampeni n’kusintha mawanga zikawayendera.

“Anthutu amafuna zotsatira osangoti kankheni kenako mukakwera mmwamba ubale watha. Pokhapokha khalidwe lotereli litasintha, vuto lothawa kuvota silingathe,” adatero Dulani.

Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe okhudzidwa ndi zisankho wa Malawi Electoral Support Network (Mesn), Steve Duwa, adati ichi n’chizindikiro choti anthu adataya chidwi ndi zisankho.

Iye adati palibe chomwe chingalimbikitse anthu kukaponya voti pomwe nthawi ndi nthawi amakhumudwitsidwa ndi atsogoleri omwe adawasankha, makamaka pakayendetsedwe ka zinthu.

Ndanga: Izi zadutsa  tiyang’ane zakutsogolo
Ndanga: Izi zadutsa
tiyang’ane zakutsogolo

“Vuto lalikulu n’kusaganizira anthu omwe amaponya voti. Anthuwa amakhala ndi zambiri zochita koma amalolera kuzisiya kuti akaponye voti ndi chiyembekezo choti atumikiridwa bwino, ndiye zikapanda kuyenda momwe amayembekezera, zotsatira zake zimakhala zimenezi,” adatero Duwa.

Mfundozi zidagwirizana ndi zomwe Tamvani wapeza kuchokera kwa anthu osiyanasiyana omwe akuti adatopa n’kuika anthu m’mpipando koma mapeto ake n’kulandira chipongwe.

“Tikaunika bwinobwino, timaona kuti zomwe timauzidwa pakampeni si zomwe timaona zisankho zikapita ndiye pena pake munthu umalingalira kuti bola nthawi yako uigwiritse ntchito ina,” adatero Adam Potani, wochokera kwa Kaliyeka.

Naye Maria Silungwe wa ku Nchezi ku Lilongwe, adali ndi ndemanga yomweyo koma iye adawonjezera kuti andale ena akasankhidwa amafuna kuti anthu omwe adawasankhawo ndiwo aziwatumikira mmalo moti iwo ndiwo azitumikira anthuwo.

Chisankho chisadachitike, Tamvani adacheza ndi zipani zonse zomwe zimapikisana nawo ndipo zotsatira zidasonyeza kuti chipani chilichonse chidali ndi chiyembekezo chotenga mipando yonse.

Chitatha chisankho, tidafunsanso ndemanga za zipanizi ndipo kudaoneka kuti zotsatirazi sizidasinthe maganizo a zipanizi pa za tsogolo lawo.

Mneneri wa chipani cha MCP, Alekeni Menyani, adati zotsatirazi zidasonyeza kuti chipanichi nchamphamvu chifukwa chidatenga mipando yambiri ngakhale kuti chimapikisana ndi chipani cholamula pambali pa zipani zina.

Iye adati chisankhochi chidali ngati liwiro la mumchenga loyamba mosiyana chifukwa ena adali ndi mpata wogwiritsa ntchito zipangizo za boma nthawi ya kampeni pomwe zina amadalira m’thumba mwawo.

Mneneri wa chipani cha DPP, Francis Kasaira, adati chipanichi chidachita chamuna chifukwa chidapita kumpikisanowu chitataya makhansala ake awiri ndipo chidakwanitsa kupezanso makhansala ena awiri kutanthauza kuti mphamvu sizidasinthe.

Ken Ndanga wa chipani cha UDF adati madzi apita ndipo kwatsala tsopano n’kuunika pomwe chipanichi chidafooka kuti zomwe zachitika ulendo uno sizadzachitikenso mtsogolo.

Tidayesetsa kuti amve maganizo a chipani cha PP koma wogwirizira mpando wa mtsogoleri wa chipanichi, Uladi Mussa, sadayankhe foni yake yam’manja maulendo angapo.

Ngati sipangaonekenso ngozi ina kapena wina kutula pansi udindo wake, ndiye kuti chisankho china chidzakhalako m’chaka cha 2019 pomwe Amalawi adzasankhe mtsogoleri wa dziko, aphungu a Nyumba ya Malamulo komanso makhansala.

Related Articles

Back to top button
Translate »