Nkhani

Kusowa kwa madzi kusokoneza zambiri ku Lilongwe

Listen to this article

Chidziwitso cha Lilongwe Water Board (LWB), bungwe lopopa ndi kugawa madzi mumzinda wa Lilongwe, choti madzi akhala akuvuta kufikira dzinja chatsimikiza kuti ntchito zambiri, makamaka za umoyo, zisokonekera mumzindawu, womwe ndi likulu la dziko la Malawi.

LWB idalengeza sabata ziwiri zapitazo kuti iyamba kugawa madzi mosinira potengera mlingo wa madzi womwe kampaniyi ili nawo m’madamu ake awiri a Kamuzu 1 ndi 2.

Some of the residents that went to draw water at Madzi House
Bungweli lidati pomwe madera ena azilandira madzi mumzindawu, kwina kuzikhala kopanda madzi ndipo izi zipitirira mpakana mvula ya chaka chamawa idzabwere.

“Kuvuta kwa mvula kwachititsa kuti madzi achepe modetsa nkhawa m’madamu awiri a Kamuzu 1 ndi 2 omwe timasungiramo madzi. Madzi omwe alipo panopa sangapose theka la madzi omwe timafuna kuti tikwaniritse ntchito yathu,” chidatero chikalata cha bungweli.

Madamuwa alibe madzi okwanira kaamba koti mvula sidagwe bwino komanso mitengo yomwe imathandiza kusunga madzi idatha mmphepete mwa mtsinje wa Lilongwe.

“Timadalira madzi ochokera mumtsinje wa Lilongwe womwe umatsira m’madamu athu. Mtsinjewu umachokera m’nkhalango ya Dzalanyama koma poti mitengo idatha m’nkhalangomu, mtsinjewu uli pambalambanda ndiye madzi sachedwa kuuma,” chidatero chikalatachi.

Mneneri wa chipatala chachikulu mumzindawu cha Kamuzu Central Hospital (KCH), Mable Chinkhata adati ngakhale kuti madziwo sadayambe kuvuta pachipatalachi, ali ndi nkhawa kuti zidzatha bwanji madzi akadzayamba kuvuta chifukwa ntchito zambiri pachipatalachi zidzasokonekera

“Ntchito zaumoyo, makamaka pachipatala, zimafuna madzi kwambiri. Mwachitsanzo, makina omwe timachapira zipangizo zochitira opaleshoni ngakhaleso zochapira zogonera ndi zofunda kapena makatani zimasiya kugwira ntchito madzi akangosiya chifukwa zimayendera kompyuta,” adatero Chinkhata.

Iye adati makinawa salola madzi ochita kuthiramo, koma opopa okha kudzera m’makina a kompyuta, ndiye madzi akangosiya makinawa nawo amasiya kugwira ntchito.

Chinkhata adati nkhani ina yomwe ingavute ndi yaukhondo potengera kuti pachipatalachi palibe zimbudzi zokwanira zokumba moti odwala ndi owadikirira omwe amadalira zimbudzi zamadzi.

“Timasunga odwala pafupifupi 1 000 patsiku ndiye ena pomwepo amakhala ndi owadikirira awiri kapena atatu. Mukawerengera ndi anthu angati amenewo? Tsono onse azigwiritsa ntchito zimbudzi zamadzi, chonsecho madziwo palibe, sikubala mavuto ena kumeneku?” adatero Chinkhata.

Vutoli ndi lomweso anthu okhala mumzindawu omwe amagwiritsa ntchito zimbudzi za madzi aona ndipo ali nalo mantha kuti likhoza kubutsa matenda osiyanasiyana n’kusokoneza ntchito zambiri.

“Tangoganizani pamalo poti pali zimbudzi zamadzi zokhazokha popanda chokumba anthu akamva mmimba azipita kuti madzi atasowa kwa masiku awiri? Mapeto ake anthu akhoza kumapita mtchire kapena kungodzithandiza m’toileti n’kusiyamo choncho. Poterepa munthu mmodzi kungodwala matenda am’mimba ndiye kuti komboni yonse,” adatero Innocent Mzungu, wa ku Falls mumzindawu.

Derali ndi limodzi mwa madera omwe nyumba zambiri zili ndi zimbudzi zamadzi ndipo zidamangidwa moyandikana.

Nkhani ina yomwe vutoli likhudze ndi la ulimi poti bungwe la BWB laletsa anthu okhala kumtunda kwa mtsinje wa Lilongwe omwe umatsira madzi m’madamu awo kuchita ulimi wamthirira.

Apa zikukolana ndi ganizo la boma loti anthu achilimike paulimi wamthirira polingalira kuti kakololedwe ka chaka chino sikadayende bwino, koma mlembi wamkulu muunduna wa zamalimidwe, Erica Maganga, adati ayambe

wakambirana ndi kampaniyi kaye.

“Choyamba sitikudziwa kuti ndi anthu angati amagwiritsa ntchito madamuwa kapena mtsinje wa Lilongwe paulimi wamthirira. Ndikuyenera kuti ndikambirane ndi akuluakulu a kampaniyi kuti tione pomwe pali vuto ndi momwe tingapangire,” adatero Maganga.

Phungu wa kunyumba ya malamulo yemwe nkhalango ya Dzalanyama ili m’dera lake, Peter Dimba, adati vutoli ndilochita kuweta chifukwa m’zaka 10 mpaka 15 zapitazo atsogoleri adalibe chidwi choteteza nkhalangoyi.

Iye adati m’zakazi, mitengo yambiri idadulidwa makamaka ndi anthu owotcha makala ndi ogulitsa nkhuni ndipo pomwe akuluakulu amadzidzimuka, madzi adali atafika kale m’khosi.

“Mpanopotu pomwe zikukhala ngati akuluakulu akukhuzumuka. Muone chitumizireni asirikali ankhondo m’nkhalangoyi zinthu zikusintha. Tsono ankalekeranji kuganiza zimenezi kalelo?” adatero Dimba.

Iye adati ali ndi chikhulupiriro kuti ndi chitetezo chomwe chilipochi, chiyembekezo chili pa mphukira za mitengo kuwonjezera pa mitengo yomwe ikubzalidwa chaka ndi chaka.

Izi zili chonchi mumzindawu, makampani opopa ndi kugawa madzi m’mizinda ya Blantyre ndi Mzuzu ati iwo alibe nkhawa ina iliyonse chifukwa mitsinje ndi madamu omwe amapopamo muli madzi okwanira.

Pakalipano, mkulu wa bungwe la anthu ogula ndi kugwiritsa ntchito malonda la Consumers Association of Malawi (CAMA) John Kapito adati ichi chikhale chitsegula m’maso kwa aliyense.

Iye adati m’nyengo ino yakusintha kwa nyengo chilichonse chikhoza kuchitika ndiye mpofunika kuti mabungwe opopa ndi kugawa madzi akhale ndi malo ambiri komanso odalirika osungirako madzi kupewa mavuto ngati omwe agwa mumzinda wa Lilongwe.

“Tizidziwa kuti madzi ndi moyo. Chilichonse chomwe munthu amapanga pamoyo wake chimalira madzi ndiye mpofunika kusamala kwambiri pankhani yokhudza madzi, osamachita zinthu modzidzimukira,” adatero Kapito.

Related Articles

Back to top button
Translate »