Nkhani

Kwezani ndalama ku umoyo—MHEN

Listen to this article

Mavuto a zaumoyo m’Malawi muno ndiye ndi osayamba. Odwala kuthinana m’zipatala, mankhwala kusowa, madotolo ochepa komanso zipatala zotalikana. Mkulu wa bungwe la Malawi Health Equity Network (Mhen) George Jobe, wati mavuto onsewa akudza chifukwa dziko lino silikuyika K15 ya K100 ya ndondomeko ya zachuma ku ntchito zaumoyo.

Jobe adati maiko a mu Africa kuphatikizapo Malawi adasainira pangano ku Abuja mu 2001 kuti ndalama zoika ku zaumoyo zisamachepere K15 pa K100 iliyonse. Maiko adasayinira panganolo limene adalilimbikitsa ndi a bungwe loona zaumoyo padziko lonse la World Health Oragnisation (WHO).

M’zipatala zina mumakhala kuthinana kwambiri

Kafukufuku wa Tamvani, wasonyeza kuti zaka zitatu zapitazi, ndondomeko ya zachuma m’dziko muno yakhala ikupereka ndalama zosaposa K8.70 pa K100 iliyonse ndipo pandondomeko imene tikuyendera pano kudayikidwa ndalama zochepetsetsa kuposa zaka zonse.

Jobe adati izi zikudzetsa mavuto a kusowa kwa mayendedwe (ma ambulansi), chiwerengero cha ogwira ntchito, kutalikana kwa zipatala  ndi kusowa mankhwala.

“Amene adaphunzira ntchito za chipatala ambiri akusowa ntchito,” adatero Jobe.

Iye adati pmaiko adagwirizananso kuti pamayenera kukhala makilomita 8 kuchoka pachipatala china kukafika china ndipo posachedwapa mtundawu udatsitsidwa kufika pa makilomita 5 koma dziko la Malawi silikwanitsabe.

“Komanso misewu yake ndi yomvetsa chisoni zomwe zimakhudzanso nkhani ya mayendedwe. Ma ambulansi ndi osowa m’zipatala ndipo akapezeka, umva kuti palibe mafuta,” adatero iye.

Iye adati vuto lalikulu ndi kasamalidwe ndi kayendetsedwe ka ntchito poyeza ndi kupereka mankhwala kwa odwala.

“Mankhwala ena boma limagula koma ena makamaka okhudzana ndi malungo amachokera kwa maiko otithandiza omwe ali ndi malamulo awo,” adatero iye.

Iye adati athandiziwo akapereka mankhwalawo amereka limodzi ndi zida zoyezera ndiye nthawi zina chifukwa chochuluka kwa odwala, a chipatala ena sayeza, amangogwiritsa ntchito zizindikiro.

Adaonjeza: “Akabwera otithandiza, amapeza kuti mankhwala atha, koma zoyezera zikadalipo tsono amavuta kuti apereke mankhwala ena msanga.”

Mneneri wa unduna wa zaumoyo Andrian Chikumbe adalephera kupereka ndemanga pa nkhaniyi Tamvani atamugogodera kuyambira Lachiwiri.

Mneneri wa unduna wa zachuma, Alfred Kutengule, adati boma la Malawi limalephera kukwaniritsa zinthu zina chifukwa chakuchepekedwa.

“Chilungamo nchakuti mapezedwe athu ngovutirapo. Timayenera kukambirana ndi anzathu otolera misonkho kuti tiwone momwe tingagawire kochepa komwe atolelako nchifukwa chake zina timalephera,” adatero Kutengule.

Izi zili choncho, Amalawi ndi amene akusautsika kwambiri, patatha zaka zoposa 50 chilandirire ufulu wathu.

Ena mwa anthu amene tidacheza nawo adandaula za kuthinana kuchipatala, kusowa mankhwala, kuyenda mtunda wautali ngati ena mwa mavuto amene amakumana nawo. 

Related Articles

Back to top button
Translate »