Nkhani

Mafuta atsika koma katundu sakutsika mtengo

Listen to this article

Bungwe loona ufulu wa ogula la consumers association of malawi (cama) lati likukonza zomema amalawi kuti anyanyale kugula katundu wodula m’sitolo kapena kukwera minibasi ngati njira yokakamiza eni bizinesi kuti atsitse mitengo ya katundu wawo kutsatira kutsika mtengo kwa mafuta monga petulo, dizilo ndi anyale.

Ganizo la bungweli likudza bungwe la malawi energy regulatory authority (mera) litatsitsa mitengo ya mafutawa kawiri m’miyezi ya january ndi february.

Motorists will soon start buying ethanol at service stations

Ngakhale mafutawa atsika mtengo, mitengo ya katundu njobowolabe m’thumba. Si katundu yekha, nayo mitengo ya maulendo idakali yokwera, chimodzimodzinso kuzigayo.

Izitu zikusemphana ndi zomwe zimachitika mafuta akakwera mtengo, pamene katundu ndi mitengo ya maulendo imakwera pakutha pa tsiku lomwe alengeza za kukwera kwa mafutawo. Kodi zikomere mbuzi kugunda galu?

Mkulu wa bungwe la cama john kapito akuti ayi zisatero ndipo wayamba kale kuthamangathamanga kuti akonze zonyanyala pofuna kukakamiza mbalizi kuti zitsitse mitengo.

Kapito akukhulupirira kuti ngati patakhala komiti yoona za mitengo momwe ilili, ogula sangalire monga zilili pano.

Gawo lina la lamulo limene lidakhazikitsidwa mu 2003 loteteza ogula la consumer protection act muli chikonzero chokhazikitsa komiti yomwe iziona momwe mitengo ikuyendera.

“Tikulankhula ndi a ofesi ya pulezidenti ndi nduna zake pa zokhala ndi komitiyi. Titakhala nayo, sitingamavutike chonchi,” adatero kapito.

Iye adati pamene kulankhulanako kuli mkati, iye limodzi ndi a bungwe lake ayamba kuyenda kuona momwe mitengo ilili ndipo pakutha pa sabata ziwiri akhala atamaliza ndipo ngati zinthu sizisintha akonza zionetsero.

“Ngati sipakhala kusintha pakutha pa sabata ziwiri, ndiye tidzagwirizana ndi ogula kuti tinyanyale, tisamagulenso katundu wawo,” adatero kapito Tamvani atamufunsa zomwe bungwe lake likuganiza pa kusatsika kwa mitengo ya katundu pamene mafuta atsika.

Nanga eni basi ndi minibasi achita nawo bwanji?

Kapito adafotokoza motere: “tigwirizanso kuti tisakwere basi kapena minibasi zawo. Iwowo amakweza mitengo mafuta akangokwera, pano mafuta atsika kawiri konse koma palibe watsitsa mtengo. Tamva kuwawa ndiye tikufuna kuonetsa kuwawidwa [mtima] kwathuko.”

Kodi ganizo la kapito ndi lotheka?

Mkulu wa bungwe loona za chuma la malawi economic justice network (mejn) dalitso kubalasa akuti anthu angakhale ndi maganizo osiyanasiyana koma boma ndilo lingapereke mfundo yabwino yothana ndi nkhaniyi.

Kubalasa akuti kukhala ndi njira zoyang’anira momwe katundu akugulitsidwira pamene mafuta atsika mtengo ndi njira yokhayo yomwe ingathane ndi mavutowa.

“Pakuyenera kukhala njira yoonera kagulitsidwe ka katundu kapena kuona momwe mitengo ilili nthawi yomwe mafuta atsika mtengo. Izitu zingachitike ndi boma basi, zitachitika izi, chiyembekezo chilipo kuti mavuto ngati awa angathe,” adatero kubalasa.

Kubalasa adati mitengo ya katundu imayenera kutsika pamene mtengo wa mafuta watsika.

“Zikuchitikazi ndi kungotibera chabe. Ngati mafuta atsika mtengo, katundunso amayenera atsike. Koma nanga bwanji sizikutsika? Uku ndi kuberana,” adatero kubalasa.

Lachinayi tidalephera kulankhula pafoni ndi mkulu wa bungwe loyang’anira ochita malonda la malawi confederation of chambers of commerce and industry (mccci) chancellor kaferapanjira kuti timve maganizo ake pa nkhani yotsitsa mitengo ya katundu.

Koma lachiwiri sabata yomweyi kaferapanjira adauza imodzi mwa wailesi m’dziko muno kuti sizingatheke kuti lero ndi lero mitengo ya katundu itsike kaamba koti mtengo wa mafuta watsika.

Kaferapanjira adati mukatengera a maminibasi, si mafuta okha amene amalowa m’minibasi. Adati pali zinthu monga masipeyala, serevisi ndi zina zotero zimene eni galimoto amaziganizira akamakhazikitsa mitengo.

Koma pophera mphongo pankhaniyi, mneneri wa boma kondwani nankhumwa adavomerezana ndi ganizo loti katundu azitsika mtengo pamene mafuta atsika ndi labwino koma chofunika n’chakuti ganizoli akalikambirane aphungu a nyumba ya malamulo.

“Aphungu akuyenera kukambirana za nkhaniyi. Ndi zomvekadi kuti katundu kapena maulendo akuyenera kutsika mtengo pamene mafuta atsika chonchi. Ngati aphungu akavomereze izi, amalawi savutikanso,” adatero nankhumwa.

Pa 11 january, bungwe la mera lidatsitsa mitengo ya mafuta a petulo kuchoka pa k856.70 Kufika pa k760.40; Dizilo adatsikanso kuchoka pa k865.10 Kufika pa k785.40; Naye palafini adatsikanso, kuchoka pa k756.10 Kufika pa k678.80 Palita iliyonse

Anthu adali ndi chiyembekezo kuti mwina zinthu zitsika mitengo koma awo adali ngati maloto a chumba.

Ndipo pa 5 february bungweli lidatsitsanso mitengo ya mafutawa. Petulo adachoka pa k760.40 Kufika pa k696.30; Dizilo adatsikanso kuchoka pa k785.40 Kufika pa k705.50; Palafini adatsikiratu kuchoka pa k756.10 Kufika pa k678.80.

Related Articles

Back to top button
Translate »